Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachiwawa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachiwawa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zachiwawa?

PALI zinthu zambiri zimene zimachititsa anthu kuchita zachiwawa. Kuwonjezera pa anthu ocheza nawo, nyimbo kapena mafilimu amene timaonera kapenanso kumene timakhala, anthu amachitanso zachiwawa pa zifukwa izi:

Kukhumudwa. Nthawi zina anthu amene akuponderezedwa, kusalidwa, amene ali pa umphawi kapena amene mavuto awachulukira, amakhumudwa n’kuyamba kuchita zachiwawa.

Kutsatira zimene gulu likuchita. Zimene zimachitika pa masewera osiyanasiyana zimasonyeza kuti anthu akakhala pagulu amakonda kuchita zinthu zoipa. Buku lina linanena kuti zimenezi zimachitika chifukwa chakuti “anthu akakhala pagulu, ngati kumpira, samaganiza bwino moti sachedwa kuchita zachiwawa.” (Social Psychology) Kafukufuku wina anasonyezanso kuti anthu oterewa amangochita zinthu m’chigulu ndipo “saganiza mwanzeru.”

Chidani komanso nsanje. Munthu woyambirira kupha mnzake anali Kaini. (Genesis 4:1-8) Iye anapha m’bale wake chifukwa chopsa mtima komanso nsanje. Mulungu anamuuza kuti amudalitsa akasintha n’kuchita zabwino koma Kaini anaphabe m’bale wake. Zimene zinachitikira Kaini zimatithandiza kumvetsa mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.”—Yakobo 3:16.

Mankhwala osokoneza bongo komanso kuledzera. Kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kumachititsa kuti munthu adwale komanso kuti mutu wake usamayende bwino. Zimenezi zimachititsa kuti azichita zachiwawa komanso azikhala waukali.

Kusapereka chilango chokhwima. Lemba la Mlaliki 8:11 limati: “Popeza anthu ochita zoipa sanalangidwe msanga, n’chifukwa chake mtima wa ana a anthu wakhazikika pa kuchita zoipa.” Dziko likakhala kuti lilibe malamulo okhwima komanso ngati anthu oyendetsa milandu sadziwa bwino ntchito yawo kapena ndi achinyengo, anthu amangochita zachiwawa mopanda mantha.

Chipembedzo chonyenga. Nthawi zambiri zipembedzo ndi zimene zimalimbikitsa zachiwawa, zauchigawenga komanso kuti anthu azichitira zachiwawa anthu a zipembedzo zina. Mwachitsanzo, pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, asilikali achipembedzo chimodzi ankaphana chifukwa chosiyana mayiko ndipo nthawi zambiri atsogoleri awo ankawadalitsa asanapite kunkhondo. Mulungu amadana ndi zimenezi.—Tito 1:16; Chivumbulutso 17:5, 6; 18:24.

Popeza kuti pali zinthu zambiri zimene zimalimbikitsa zachiwawa, kodi ndi zotheka kukhala munthu wokonda mtendere? Inde n’zotheka monga tionere m’nkhani yotsatira.

[Bokosi patsamba 6]

CHIWAWA CHIMAYAMBIRA MUMTIMA

N’zoona kuti pali zinthu zambiri zimene zimachititsa kuti munthu ayambe zachiwawa, komabe chiwawa chimayambira mtima. Mwachitsanzo, Yesu Khristu, yemwe ankadziwa kwambiri zimene zili mumtima mwa munthu, anati: “Pakuti mkatimo, mumtima mwa munthu, mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama, zakuba, zaumbanda, zachigololo, kusirira kwa nsanje, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira, diso la kaduka, mnyozo, kudzikweza, ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena.” (Maliko 7:21, 22) Munthu amayamba kukhala ndi makhalidwe amenewa akamapitiriza kuonera, kumvetsera kapena kuganizira zinthu zoipa.—Yakobo 1:14, 15.

Koma tikamaganizira zinthu zabwino, zangati zimene zatchulidwa mu nkhaniyi patsamba 8, timakhala ngati tikuchotsa maganizo oipa mumtima mwathu, n’kuikamo maganizo abwino. (Akolose 3:5; Afilipi 4:8) Tikatero, Mulungu adzatithandiza kuti “munthu [wathu] wamkati akhale wamphamvu.”—Aefeso 3:16.

[Bokosi patsamba 7]

AKATSWIRI AIMA MUTU NDI ZACHIWAWA

Anthu ambiri amadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani chiwerengero cha anthu ophedwa ndi anthu anzawo n’chokwera kwambiri m’mayiko ena? N’chifukwa chiyani nkhondo komanso zachiwawa zikupitirirabe kuchitika?’ Palinso mafunso ambiri amene anthu amalephera kupeza mayankho ake.

Akatswiri ena amanena kuti anthu amachita zachiwawa chifukwa choti ena amawasala komanso chifukwa cha umphawi. Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse amene amaphedwa kapena kudzipha, amakhala a m’mayiko osauka. Kafukufukuyo anasonyezanso kuti m’mizinda imene mumakhala anthu osauka ndi mmene mumachitika zachiwawa kwambiri. Koma kodi n’zoona kuti anthu osauka ndi amene amakhala achiwawa kwambiri? Kapena kodi m’madera amenewa mumachitika zachiwawa chifukwa chakuti achitetezo sagwira ntchito yawo mokwanira? Mwachitsanzo, taganizirani za mzinda wa Calcutta, womwe uli ku India. Ngakhale kuti mzindawu uli ndi anthu osauka kwambiri koma ndi umodzi mwa mizinda yomwe simuchitika zachiwawa pafupipafupi.

Ena amanena kuti anthu amakonda kuchita zachiwawa m’mayiko amene anthu wamba amapeza mfuti mosavuta. N’zoona kuti anthu achiwawa akakhala ndi mfuti akhoza kuchita zinthu zoopsa. Koma funso lina n’lakuti, N’chifukwa chiyani m’madera ena muli anthu ambiri okonda zachiwawa? Pa mfundo imeneyinso, akatswiri amanena maganizo osiyanasiyana.