Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndimatengera Chitsanzo cha Ndani?

Kodi Ndimatengera Chitsanzo cha Ndani?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndimatengera Chitsanzo cha Ndani?

Mu nkhani ino, mudziwa

CHIFUKWA chake muyenera kutengera zitsanzo za anthu ena

KUMENE mungapeze zitsanzo zabwino

ZIMENE mungachite kuti mutengere chitsanzo chawo

CHIFUKWA CHAKE MUYENERA KUTENGERA ZITSANZO ZA ANTHU ENA

DZIWANI IZI: Nthawi zambiri munthu amatengera khalidwe la anthu amene amawasirira. Akhoza kutengera khalidwe labwino kapena loipa, zimangodalira anthu amene akuwatengerawo.

Zimene mumafunikira: Anthu a makhalidwe abwino amene mungatengere chitsanzo chawo.—Afilipi 3:17.

Vuto: Anthu ambiri amatengera khalidwe la anthu otchuka monga oimba, akatswiri amasewera kapena anthu a m’mafilimu. Iwo amachita zimenezi ngakhale kuti anthuwo amachita zinthu zoipa.

Mfundo yoti muzikumbukira: Baibulo limayerekezera makhalidwe athu ndi chovala. (Akolose 3:9, 10) Tiyerekeze kuti munthu wina yemwe wavala zovala zosaoneka bwino komanso zakuda akukupatsani zovala zakezo kuti muvale, kodi mungalandire? N’zodziwikiratu kuti simungalole. Mofanana ndi zimenezi, munthu wanzeru zake sangalole kuti azitengera makhalidwe a munthu winawake wotchuka, yemwenso ali ndi mbiri yoipa. M’malo mongotsatira zimene anthu ambiri amachita, mungachite bwino kukhala ndi anthu omwe mumawaona kuti ndi zitsanzo za makhalidwe abwino. Zimenezi zingakuthandizeni kuti (1) mudziwe makhalidwe amene mukufuna kukhala nawo komanso kuti (2) muzitsanzira anthu amene amayesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mukufunawo.

KUMENE MUNGAPEZE ZITSANZO ZABWINO

Chongani ngati mfundo zotsatirazi zili zoona kapena zonama.

1. Muyenera kutengera chitsanzo cha munthu yekhayo amene munaonanapo naye maso ndi maso.

Zoona Zonama

2. Muyenera kutengera chitsanzo cha munthu amene sanalakwitsepo chilichonse.

Zoona Zonama

3. Mukhoza kutengera zitsanzo za anthu ambirimbiri.

Zoona Zonama

Mayankho

1. Zonama. Mukhoza kusankha zitsanzo za anthu akale kwambiri ndipo ambiri mwa anthu amenewa amapezeka m’Baibulo. Mwachitsanzo, mutawerenga Aheberi chaputala 11, muona kuti mtumwi Paulo anatchula amuna ndi akazi okwana 16, omwe ndi zitsanzo zabwino pa nkhani ya chikhulupiriro. Koma chitsanzo chabwino kwambiri ndi chimene Paulo anachifotokoza mu chaputala 12. Iye analimbikitsa Akhristu kuti ‘ayang’anitsitse’ pa Yesu n’kutengera chitsanzo chake. (Aheberi 12:2) Zimenezi zikusonyeza kuti munthu wabwino kwambiri amene tingatengere chitsanzo chake ndi Yesu.—Yohane 13:15. *

2. Zonama. Kupatulapo Yesu, palibe mbadwa ya Adamu imene ili yangwiro. (Aroma 3:23) Ngakhale kuti mneneri Eliya anachita zozizwitsa, iye “anali munthu monga ife tomwe.” (Yakobo 5:17) Ndi mmenenso zinalili ndi anthu monga Miriamu, Davide, Yona, Malita ndi Petulo. Baibulo limanena mosabisa zimene anthuwa analakwitsa, komabe anali ndi makhalidwe abwino kwambiri omwe munthu angatengere.

3. Zoona. Munthu akhoza kutengera zitsanzo zabwino za anthu ambirimbiri mmene angafunire. Mwachitsanzo, mukhoza kutengera zitsanzo za anthu atatu. Woyamba akhoza kukhala wolimbikira ntchito, wina akhoza kukhala woleza mtima ndipo winayo akhoza kukhala wolimba mtima ngakhale akumane ndi mavuto. (1 Akorinto 12:28; Aefeso 4:11, 12) Nthawi zonse muziyesetsa kuona makhalidwe abwino a anthu ena ndipo mudzapeza kuti ali ndi makhalidwe amene mungatengere.—Afilipi 2:3.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUTENGERE CHITSANZO CHAWO

1. Muzionetsetsa mmene amachitira zinthu. Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Muzionetsetsa amene akuyenda mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani.”Afilipi 3:17.

2. Muzicheza nawo. Ngati n’zotheka, muziyesetsa kucheza ndi anthu amene mwawasankha kuti mutengere chitsanzo chawo. Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”—Miyambo 13:20.

3. Muzitsanzira makhalidwe awo abwino. Lemba la Aheberi 13:7 limati: “Pamene mukuonetsetsa zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.”

Ngati mwakonzeka kusankha munthu amene mukufuna kutengera chitsanzo chake, tsatirani malangizo ali m’munsiwa.

Zoti Muchite

Sankhani khalidwe limene mukufuna kutengera. (Kodi mukufuna kuti muzikhala womasuka kucheza ndi anthu? wopatsa? wolimbikira ntchito? wololera? wodalirika? kapena wokhulupirika?)

․․․․․

Sankhani munthu amene mukuona kuti ali ndi khalidwe limene mumafuna mutakhala nalo. *

․․․․․

Sikuti cholinga chanu ndi choti musinthe n’kumachita zinthu zofanana ndendende ndi munthu winayo. Inunso panokha muli ndi makhalidwe abwino. Komabe kukhala ndi anthu azitsanzo zabwino amene mungatengere khalidwe lawo, kungakuthandizeni kuti mukule ndi makhalidwe abwino. Komanso mukamatengera chitsanzo chabwino cha anthu ena, inunso mumakhala chitsanzo chabwino kwa ena.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Masiku anonso kuli anthu amakhalidwe abwino amene mungatengere chitsanzo chawo. Anthu amenewa akhoza kukhala makolo, achibale kapena Akhristu anzanu omwe amakonda kwambiri Mulungu. Mukhozanso kutengera chitsanzo cha m’bale kapena mlongo wamakhalidwe abwino amene mukumudziwa kapena amene munawerengapo nkhani yake.

^ ndime 32 Mukhozanso kuyamba ndi kusankha munthu amene mumamusirira. Mukamusankha dzifunseni kuti, ‘Kodi munthuyu ali ndi khalidwe liti limene ndimafuna nditakhala nalo?’ Kenako, yesetsani kutengera khalidwelo.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Munthu wanzeru sangalole kuti azitengera makhalidwe a munthu winawake wotchuka, yemwenso ali ndi mbiri yoipa

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 22, 23]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Layla—Ndili ndi mnzanga, dzina lake Sandra. Iye amati akakumana ndi mavuto sada nkhawa kwambiri. Amadziwanso Baibulo kwambiri moti savutika kupeza njira zothanirana ndi mavuto osiyanasiyana. Ineyo ndikakhala ndi vuto lililonse ndimamuuza.

Terrence—Ndili ndi anzanga awiri, mayina awo ndi Kyle ndi David. Iwo amaona kuti maganizo a wina aliyense ndi ofunika. Komanso ndi osadzikonda chifukwa amasiya mavuto awo kuti athandize anthu ena. Ndimafuna kutengera makhalidwe amenewo.

Emmaline—Ndimatengera chitsanzo chabwino cha mayi anga. Amadziwa Baibulo kwambiri ndipo amayesetsa kupeza mpata woti auze ena zimene amakhulupirira. Iwo amaona kuti kulalikira ndi mwayi waukulu, osati chintchito chotopetsa. Ndimawasirira kwambiri chifukwa cha zimenezi.

[Bokosi patsamba 23]

MUKAFUNA KUPEZA MFUNDO ZINA

Kodi mukufuna mfundo zina zokuthandizani kupeza anthu a zitsanzo zabwino? Werengani Aheberi chaputala 11, ndipo sankhani munthu m’modzi kapena awiri amene awatchula m’chaputalachi. Kenako muziyesetsa kupeza nthawi yophunzira zambiri za munthuyo n’cholinga choti mutengere chitsanzo chake chabwino.

Mukhozanso kupeza zitsanzo zina za m’Baibulo m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Onani mutu wakuti “Zitsanzo Zabwino,” mkati mwa chikuto cha kumapeto kwa bukuli.

[Bokosi patsamba 23]

FUNSANI MAKOLO ANU

Afunseni makolo anu za anthu amene iwowo ankatengera chitsanzo chawo ali achinyamata. Afunseninso kuti akuuzeni zitsanzo zimene amatengera panopa. Apempheni kuti akuuzeni zimene apindula chifukwa chotengera chitsanzo chabwino cha anthu ena.