Onani zimene zilipo

NKHANI YA PACIKUTO

Kuseŵenzetsa Nthawi Yanu Mwanzelu

Kuseŵenzetsa Nthawi Yanu Mwanzelu

Nthawi zambili anthufe timanena kuti: “Nikanakhala na nthawi nikanacita zakuti-zakuti.” Kunena zoona palibe amene ali na nthawi yoculuka kuposa mnzake. Cifukwa anthu olemela na osauka omwe, ali na nthawi yofanana. Komanso, anthu olemela na osauka akhoza kupeza nthawi posacita zinthu zosafunika kwenikweni. Nthawi ikadutsa, sibwelelanso. Conco, ni nzelu kugwilitsa nchito bwino nthawi yomwe tili nayo. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Taonani zinthu 4 zotsatilazi zomwe zathandiza anthu ambili kuti azigwilitsa nchito bwino nthawi yawo.

Njila Yoyamba: Muzicita Zinthu Mwadongosolo

Muziyamba na zinthu zofunika kwambili. Baibo imatilangiza kuti: “Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Tsiku lililonse m’mawa, ganizilani zinthu zimene mukufuna kucita pa tsikulo. Ndiyeno ganizilani zofunika kwambili kapena zoyenela kucitidwa mwamsanga. Koma muzikumbukila kuti zinthu zina zikhoza kukhala zofunika kwambili, koma si zofunika kuzicita nthawi yomweyo. Mwacitsanzo, kuphika cakudya camasana n’kofunika kwambili, koma simungacite zimenezi mutangouka. Komanso, kuonela pulogalamu inayake pa TV kapena kumvela pulogalamu inayake ya pa wailesi, kungafune kuti mucite zimenezo pa nthawi imene pulogalamuyo imaonetsedwa kapena kuulutsidwa. Komatu zimenezi si zofunika kwambili. *

Muzikonzekelelatu zimene mukufuna kucita. Lemba la Mlaliki 10:10 limati: “Ngati nkhwangwa yabuntha ndipo munthu sanainole, adzawononga mphamvu zake pacabe.” Limatinso: “Kugwilitsa nchito bwino nzelu kumapindulitsa.” Kodi tikuphunzilapo ciani pamenepa? Kukonzekelelatu zinthu, komwe kuli ngati kunola nkhwangwa, kungathandize kuti musawononge nthawi yaitali pocita zinthuzo. Komanso pocita zinthu, musamayambe na zinthu zosafunika kwenikweni, apo ayi, muzingozisiya, cifukwa zinthu zotelezi zingangokuwonongelani nthawi na mphamvu zanu. Ngati mwaona kuti muli na nthawi cifukwa coti mwamaliza msanga kucita zinazake, yambani kucita zina zimene munakonza kuti muzicite pa nthawi ina. Mukamakonzekelelatu zocita, mumakhala ngati munthu amene wanolelatu nkhwangwa yake asanayambe kuigwilitsa nchito, ndipo izi zingacititse kuti muzicita zinthu zambili pa tsiku.

Musamadziculukitsile zocita. Musamathe nthawi yanu yambili pa zinthu zosafunika kwenikweni kapenanso zosafunika n’komwe, zomwe zingangokuwonongelani nthawi. Kudziculukitsila zocita kungapangitse kuti muzikhala na nkhawa komanso wosasangalala.

Njila Yaciŵili: Muzipewa Zinthu Zimene Zingakuwonongeleni Nthawi

Kuzengeleza ndiponso kulephela kusankha zocita. Lemba la Mlaliki 11:4 limati: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” Kodi tikuphunzila ciani palembali? Kuzengeleza kucita zinthu kungatiwonongele nthawi komanso sitingacite zambili pa tsiku. Mlimi amene amayembekezela kuti zinthu zonse zikhale bwino asanayambe kulima, sangabzale komanso kudzakolola mbewu zake. Conco tisamalole zinthu zosayembekezeleka pamoyo kutipangitsa kuti tilephele kusankha zocita. Kapena tingaone kuti tiyenela kuyembekezela mpaka titapeza mfundo zonse zimene tikufuna tisanasankhe zocita. N’zoona kuti, tisanasankhe zocita pa zinthu zofunika kwambili, coyamba tiyenela kuganizila kwambili nkhaniyo komanso kufufuza zinthu zina. Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.” Komabe tiyenela kudziŵa kuti pali zinthu zina zoti sitingazidziŵiletu. Conco tisamalephele kusankha zocita cifukwa ca zinthu ngati zimenezi.—Mlaliki 11:6.

Kufuna kucita zinthu mosalakwitsa. Lemba la Yakobo 3:17 limati: “Nzelu yocokela kumwamba, [kapena kuti kwa Mulungu] . . . ndi yoyela.” N’zoona kuti aliyense amafuna kuti azicita bwino zinthu. Komabe kuganizila kwambili zimenezi kungacititse kuti tizifunitsitsa kucita ciliconse popanda kulakwitsa, ndipo zimenezi zingangocititsa kuti tizikhala okhumudwa nthawi zonse. Mwacitsanzo, munthu amene akuphunzila cinenelo cina sayenela kukhumudwa akalakwitsa. Ayenela kudziŵa kuti zimenezo zingamuthandize kuti aphunzilepo kanthu. Koma munthu amene amafuna kucita zinthu mosalakwitsa, akhoza kulephela kulankhula cinenelo catsopano cifukwa coopa kulakwitsa. Conco ni bwino kukhala odzicepetsa pocita zinthu. Lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.” Ndipotu anthu odzicepetsa sadziganizila kwambili. Ndipo anthu akamawaseka pa zimene alakwitsa, sadandaula nazo.

“Kuti tipeze cinthu, sikuti timakhala kuti tagwilitsa nchito ndalama zokha. Timakhalanso kuti tagwilitsa nchito nthawi.”—What to Do Between Birth and Death

Njila Yacitatu: Musamacite Zinthu Monyanya

Muzipezanso nthawi yocita zosangalatsa. “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Anthu amene amagwila nchito monyanya, nthawi zambili sakhala na mpata wosangalala na zotsatila za nchito yawoyo cifukwa nthawi zonse amangokhala otopa. Pamene anthu aulesi nawonso, m’malo moti azigwila nchito amawononga nthawi pa zinthu zosafunika. Koma Baibo imatilangiza kuti tisamagwile nchito monyanya komanso tisakhale aulesi. Imati tiyenela kugwila nchito mwakhama n’kusangalala na zotsatila za nchito yathuyo. Kusangalala koteloko ni “mphatso yocokela kwa Mulungu.”—Mlaliki 5:19.

Muzigona Mokwanila. Munthu wina amene analemba nawo Baibo ananena kuti: “Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendele.” (Salimo 4:8) Nthawi zambili munthu wamkulu amafunika kugona maola 8 kuti thupi lake lizigwila nchito bwino. Kugona mokwanila n’kofunika kwambili cifukwa kumathandiza kuti munthu azitha kukumbukila zinthu komanso kuti aziphunzila zinthu msanga. Conco kugona sikuwononga nthawi. Munthu amene sagona mokwanila saphunzila msanga zinthu, angathe kucita ngozi, sacedwa kukhumudwa komanso amalakwitsa zinthu.

Muzikhala na zolinga zimene mungazikwanilitsedi. Baibo imati: “Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.” (Mlaliki 6:9) Apa mfundo ni yoti, munthu wanzelu salola kuti azingotsogoleledwa na zolakalaka za mtima wake, maka-maka zimene sangazikwanitse kapenanso sizingacitike n’komwe. Conco satengeka ni zomwe otsatsa malonda amanena kapena kutengeka na zakuti atha kupeza ngongole mosavuta. M’malomwake amaganizila kwambili zinthu zimene angathedi kuzipeza, kapena kuti zimene ‘amaziona na maso ake.’

Njila ya 4: Muziyendela Mfundo za Makhalidwe Abwino

Ganizilani mfundo zimene mumayendela. Kuti muone kuti cinthu ici ni cabwino, cofunika komanso coyenela kuwonongelapo nthawi, zimadalila mfundo zimene mumayendela. Ngati pali cinthu cinacake cimene mukufuna kukwanilitsa pa moyo wanu, mfundo zimene mumayendela zimakhala zogwilizana na colinga cimeneco. Conco, ngati mumayendela mfundo zabwino, zingakuthandizeni kuti muzicita zinthu zofunika kwambili komanso kuti nthawi zonse, muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu. Kodi mfundo zimenezi mungazipeze kuti? Anthu ambili amaona kuti mfundo zotelezi zimapezeka m’Baibo.—Miyambo 2:6, 7.

Khalidwe lanu lalikulu lizikhala cikondi. Lemba la Akolose 3:14 limanena kuti cikondi “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” Kuti tikhaledi osangalala maka-maka m’banja, tiyenela kukhala na cikondi. Anthu amene amanyalanyaza mfundo imeneyi, n’kumangoganizila kwambili nchito yawo kapena kupeza cuma, amakhala osasangalala. N’cifukwa cake Baibo imanena kuti khalidwe lofunika kwambili ni cikondi, ndipo imachula khalidweli kambili-mbili.—1 Akorinto 13:1-3; 1 Yohane 4:8.

Muzipeza nthawi yocita zinthu zauzimu. Munthu wina, dzina lake Geoff, ali na mkazi wabwino, ana aŵili, anzake abwino komanso nchito yabwino ya kucipatala. Koma akamagwila nchito yakeyi anali kuona anthu akuvutika komanso kumwalila. Iye anali kudzifunsa kuti: “Kodi umu ni mmene moyo uyenela kukhalila?” Ndiye tsiku lina anaŵelenga magazini othandiza kuphunzila Baibo omwe amafalitsidwa na Mboni za Yehova, ndipo anapeza mayankho ogwila mtima.

Geoff anafotokozela mkazi wake komanso ana ake zimene anaŵelenga m’magaziniwo, ndipo nawonso anacita cidwi. Banjali linayamba kuphunzila Baibo ndipo zimenezi zinathandiza kuti azisangalala kwambili komanso kuti azigwilitsa nchito bwino nthawi yawo. Kuphunzila Baibo kunawathandizanso kukhala na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha m’dziko limene simudzakhala mavuto alionse.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Zimene zinacitikila Geoff zikutikumbutsa mawu a Yesu Khristu akuti: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Inunso mungacite bwino kumapeza nthawi yocita zinthu zauzimu. Kunena zoona, palibe njila yabwino yogwilitsa nchito nthawi kuposa kucita zimenezi. Izi zidzakuthandizani kuti mukhale na moyo wabwino.

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti, “Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala na Nthawi Yokwanila” mu Galamukani! ya April 2010.