Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Misozi Yathu Ndi Yodabwitsa Kwambiri

Misozi Yathu Ndi Yodabwitsa Kwambiri

ANTHUFE timalira kungochokera pa tsiku limene tinabadwa. Katswiri wina ananena kuti kulira kumathandiza kwambiri ana, chifuwa ndi njira imene amanenera zimene akufuna ndipo zimathandiza kuti apezedi zimene akufunazo. Nanga n’chifukwa chiyani anthufe timalirabe tikakula, ngakhale kuti tingathe kuuza anthu zomwe tikufuna pogwiritsa ntchito njira zina?

Pali zifukwa zosiyanasiyana zomwe zimachititsa anthufe kulira. Tingalire chifukwa cha chisoni, kukhumudwa kapena chifukwa choti tikumva ululu winawake. Koma nthawi zina timalira chifukwa choti tasangalala ndi zinthu zinazake ndipo imeneyi imakhala misozi ya chisangalalo. Nthawi zina, kulira amapatsirana. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake María, anati: “Ndikaona munthu akulira, nanenso ndimayamba kulira. Kaya munthuyo akulira chiyani, ndimalephera kudzigwira kuti ndisalire.” Anthu enanso amalira akaonera filimu kapena kuwerenga nkhani inayake yomvetsa chisoni.

Kaya kulira kwabwera pa chifukwa chanji, munthu amatha kusonyeza mmene akumvera polira. Buku lina linanena kuti: “Pali zinthu zochepa kwambiri zimene zingathandize munthu kuuza anthu mmene akumvera popanda kulankhula zambiri, ngati mmene kulira kumachitira.” (Adult Crying) Anthu ambiri akaona munthu akulira, amakhudzidwa mtima kwambiri. Mwachitsanzo, ambirife tikamva munthu akulira momvetsa chisoni, timalephera kuugwira mtima chifukwa timadziwa kuti chinachake sichili bwino. Timayesetsa kuti timutonthoze kapena kumuthandiza munthu amene akulirayo.

Akatswiri ena amakhulupirira kuti kulira kumathandiza kuti munthu amveko bwino, pamene kudzigwira kwa nthawi yaitali osalira, kungawononge thanzi la munthu. Koma akatswiri ena amati asayansi sanapeze umboni wotsimikizirika wosonyeza ubwino wolira kapena kuipa kwa kusalira. Komabe kafukufuku wina anapeza kuti akazi 85 pa 100 alionse komanso amuna 73 pa 100 alionse, amayamba kumvako bwino akalira. Mtsikana wina, dzina lake Noemí anati:  “Nthawi zina ndimaona kuti ndikufunika kulira. Ndikalira, mtima wanga umakhala m’malo ndipo ndimayamba kuona zinthu moyenera.”

Kafukufuku wina anapeza kuti akazi 85 pa 100 alionse komanso amuna 73 pa 100 alionse, amayamba kumvako bwino akalira

Koma nthawi zina kulira pakokha sikuthandiza. Zimadaliranso zimene anthu ena angachite akaona kuti tikulira. Mwachitsanzo, anthu ena akaona kuti tikulira n’kutiuza mawu olimbikitsa, timamvako bwino. Koma ngati tikuona kuti anthu ena sakukhudzidwa n’komwe ndi kulira kwathuko, timachita manyazi komanso timaona kuti sakutikonda.

Apatu n’zoonekeratu kuti, misozi yathu ndi yodabwitsa kwambiri ndipo pali zambiri zimene sitikudziwa zokhudza kulira. Koma chimene tikudziwa n’choti kutulutsa misozi ndi njira imodzi imene Mulungu anatipatsa yosonyezera mmene tikumvera.