Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUDZIPHA NDI NJIRA YABWINO YOTHETSERA MAVUTO?

Pali Zimene Zingakuthandizeni

Pali Zimene Zingakuthandizeni

‘Mutulireni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’1 PETULO 5:7.

Anthu amene amaganiza kuti ndi bwino angofa, amaona kuti palibe chimene angachite kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino pa moyo wawo. Koma dziwani kuti zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni kulimbana ndi vuto lanu.

Pemphero. Sikuti pemphero limangothandiza munthu kuti mtima wake ukhale m’malo komanso sikuti timafunika kupemphera pamene zinthu zatithina basi. Pemphero ndi njira yolankhulira ndi Yehova Mulungu, amene amakukondani kwambiri. Yehova amafuna kuti muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa. Ndipotu Baibulo limatiuza kuti: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza.”—Salimo 55:22.

Choncho mungachite bwino kupemphera kwa Mulungu panopa. Popemphera muzitchula dzina lake lakuti Yehova ndipo muzimuuza zimene zili mumtima mwanu. (Salimo 62:8) Yehova amafuna kuti muzimuona kuti ndi mnzanu wapamtima. (Yesaya 55:6; Yakobo 2:23) Pemphero ndi njira yolankhulira ndi Yehova yoti mungathe kuigwiritsa ntchito nthawi iliyonse komanso kulikonse komwe muli.

Mogwirizana ndi zotsatira za kafukufuku wina, “pa anthu 100 alionse amene amadzipha, anthu oposa 90 amakhala oti anali ndi matenda a kuvutika maganizo pa nthawi yomwe anadziphayo. Koma nthawi zambiri anthuwa amakhala oti sanalandire mankhwala a matendawa chifukwa choti sanazindikire kuti akudwala matendawa”

Anthu amene amakukondani. Achibale anu komanso anzanu amakukondani ndipo mwina anasonyeza kale kuti akufuna kuti zinthu ziyambe kukuyenderani bwino. Palinso anthu ena oti mwina simukuwadziwa amene amakufunirani zabwino. Mwachitsanzo, nthawi zina a Mboni za Yehova akamalalikira kunyumba ndi nyumba, amakumana ndi anthu omwe asowa mtengo wogwira chifukwa cha mavuto, ndipo mwina akuganiza zongodzipha. Ntchito yolalikira imene a Mboni za Yehova amagwirayi imachititsa kuti akumane ndi anthu oterewa, n’kuwathandiza. Iwo amatsanzira Yesu ndipo amakonda anthu. Choncho inunso amakukondani.—Yohane 13:35.

Madokotala odziwa za matendawa. Nthawi zambiri munthu amene amaganiza zodzipha, amakhala kuti wadwala matenda a kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali. Koma dziwani kuti kuvutika maganizo n’chimodzimodzi ndi matenda ena onse, choncho palibe chifukwa chochitira manyazi ndi vutoli. Ndipotu ambiri amati matenda a kuvutika maganizo ndi ofala ngati chimfine. Choncho, aliyense angathe kudwala matenda a kuvutika maganizo. Koma ubwino wake, matendawa ali ndi mankhwala. *

MFUNDO YOYENERA KUIKUMBUKIRA: Ngati mukudwala matenda a kuvutika maganizo zimakhala ngati muli m’dzenje lakuya ndipo simungathe kutulukamo nokha. Koma anthu ena atakuthandizani, mungathe kuthetsa vuto lanulo.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA PANOPA: Pitani kwa dokotala amene amadziwa za matenda a kuvutika maganizo.

^ ndime 8 Ngati nthawi zambiri mumaganiza zodzipha, mungachite bwino kupita kuchipatala kukaonana ndi dokotala wodziwa za vutoli, kuti akuthandizeni.