Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Padziko Lonse

Bungwe lina loona za umoyo wa ana linanena kuti: “Chaka chilichonse ana pafupifupi 3 miliyoni amamwalira asanakwanitse mwezi umodzi, ndipo ambiri mwa anawa amamwalira pa zifukwa zopeweka. Ana oposa 1 miliyoni pa ana amenewa, amamwalira tsiku lomwe abadwa.”

Britain

Bungwe lina la za umoyo ku England linanena kuti mu 2011, chiwerengero cha anthu omwalira chifukwa chopuma mpweya woipa chinawonjezeka m’matauni 15 a mumzinda wa London. Ena amati dizilo ndi wosaopsa kwambiri ku thanzi la anthu chifukwa satulutsa mpweya wambiri woipa. Komabe anthu ambiri amene anafa m’matauni amenewa, anafa chifukwa cha utsi wochokera m’magalimoto oyendera dizilo.

Russia

Kafukufuku amene bungwe lina la ku Russia linachita mu 2013 anasonyeza kuti Akhristu 52 pa 100 alionse a mpingo wa Orthodox m’dzikoli, sanawerengepo Baibulo. Kafukufukuyu anasonyezanso kuti Akhristu 28 pa 100 alionse amangopemphera mwa apo ndi apo.

Africa

Lipoti la banki lalikulu padziko lonse linanena kuti kukanganirana malo olima kukuchititsa kuti ulimi usamayende bwino. Izi zikuchititsanso kuti umphawi uziwonjezeka. Hafu ya malo omwe sakulimidwa padziko lonse, yomwe ndi maekala 500 miliyoni, ali ku Africa. Koma kumeneku n’kumenenso kuli nthaka yabwino moti malo amenewa akanakhala kuti akulimidwa, bwenzi akutulutsa chakudya chambiri.

United States

Sukulu ndi yunivesite zambiri zasiya kugwiritsa ntchito mabuku ndipo zikumagwiritsa ntchito matabuleti. Ana a sukulu akumatha kuwerenga komanso kumvetsera ndi kuonera zinthu za kusukulu pogwiritsa ntchito matabuletiwa. Komabe anthu ena akukayikira ngati njirayi ili yotchipa kuyerekeza ndi kugwiritsa ntchito mabuku.