Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mayi wanzeru amatsatira chikumbumtima chake

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuchotsa Mimba

Kuchotsa Mimba

Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri amachotsa mimba. Chiwerengero cha ana osabadwa amene amaphedwa mwanjira imeneyi n’chachikulu kuposa chiwerengero cha anthu a m’mayiko ambiri.

Kodi ndi nkhani yoti munthu akhoza kungosankha yekha zochita?

ZIMENE ANTHU AMANENA

 

Azimayi amachotsa mimba pa zifukwa zosiyanasiyana. Ena amachita zimenezi chifukwa cha mavuto azachuma, kusayenda bwino kwa banja, kufuna kukhala ndi ufulu wopitiriza maphunziro kapena ntchito kapenanso chifukwa chosafuna kukhala ndi mwana wopanda bambo. Komabe anthu ena amati kuchotsa mimba n’kulakwa chifukwa amaona kuti mayi akakhala ndi mimba amakhala ndi udindo wosamalira ndiponso kuteteza mwanayo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Mulungu amaona kuti moyo, makamaka wa munthu, ndi wopatulika. (Genesis 9:6; Salimo 36:9) Izi zili choncho ngakhale kwa mwana amene akukula m’mimba mwa mayi ake, omwe ndi malo amene Mulungu anakonza kuti mwana azitetezedwa asanabadwe. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo ananena kuti: “Munali kunditchinga m’mimba mwa mayi anga. Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa.”Salimo 139:13, 16.

Tingadziwenso maganizo a Mulungu pa nkhaniyi tikaganizira Chilamulo chimene anapatsa Aisiraeli. Chilamulocho chinkanena kuti munthu amene wamenya mayi woyembekezera mpaka kupha mwana wosabadwayo nayenso ankayenera kuphedwa. (Ekisodo 21:22, 23) Komabe oweruza ankayenera kuganizira mbali zonse za nkhaniyo asanapereke chigamulo.Numeri 35:22-24, 31.

Mulungu anapatsanso anthu chikumbumtima chomwe chimawatsutsa akachita zinthu zolakwika. Mayi akatsatira zimene chikumbumtima chake chikumuuza n’kupewa kuchotsa mimba amakhala ndi mtendere wamumtima. * Koma akachinyalanyaza akhoza kusowa mtendere kwambiri. (Aroma 2:14, 15) Ndipotu kafukufuku amasonyeza kuti nthawi zambiri amayi amene achotsa mimba amakhala ndi nkhawa ndiponso amavutika maganizo.

Koma bwanji ngati mukuda nkhawa kuti mudzavutika kulera mwanayo chifukwa choti mimbayo simunaikonzekere? Taonani zimene Mulungu adzachitire anthu amene amatsatira mfundo zake mokhulupirika. Limati: “Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika. Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.” (Salimo 18:25) Limanenanso kuti: “Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.”Salimo 37:28.

“Chikumbumtima chawo chimachitira umboni pamodzi ndi iwowo, ndipo maganizo awo amawatsutsa ngakhalenso kuwavomereza.”Aroma 2:15.

Koma bwanji ngati munachotsapo mimba?

ZIMENE ANTHU AMANENA

 

Mayi wina yemwe akulera yekha ana, dzina lake Ruth, anati: “Ndinali kale ndi ana atatu ang’onoang’ono ndipo ndinkaona kuti sindingakwanitse kumasamalira ana 4. Komabe nditachotsa mimba ndinkamva kuti ndachita zinthu zoipa kwambiri.” * Koma kodi Mulungu sangamukhululukire chifukwa cha zimene anachitazi?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Zimene Yesu Khristu ananena zimasonyeza mmene Mulungu amaonera zinthu. Iye anati: “Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.” (Luka 5:32) Zimenezi zikusonyeza kuti tikamadzimvera chisoni chifukwa cha zinthu zoipa zimene tachita n’kulapa mochokera pansi pa mtima, kapena kuti kupempha Mulungu kuti atikhululukire, iye amatikhululukira ngakhale machimo athuwo atakhala aakulu. (Yesaya 1:18) Lemba la Salimo 51:17 limati: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.”

Munthu akalapa n’kupemphera mochokera pansi pa mtima, Mulungu amamuthandiza kuti asiye kudziimba mlandu komanso kuti akhale ndi mtendere wamumtima. Lemba la Afilipi 4:6, 7 limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” * Ruth, yemwe tamutchula kale uja, ataphunzira Baibulo anaona kuti ayenera kupemphera kwa Mulungu n’kulapa mochokera pansi pa mtima. Atachita zimenezi anakhala ndi mtendere wamumtima ndipo anaona kuti Mulungu ‘amakhululukadi.’Salimo 130:4.

[Mulungu] sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu, kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.”Salimo 103:10.

^ ndime 10 Si bwino kuchotsa mimba chifukwa choti dokotala wakuuzani kuti moyo wa mayi kapena wa mwana ukhoza kukhala pa ngozi. Koma ngati pa nthawi yobereka mayi ndi bambo auzidwa kuti ayenera kusankha pakati pa kupulumutsa moyo wa mayi kapena wa mwana, iwo ayenera kusankha okha zochita. Komabe masiku ano zimenezi sizichitikachitika m’mayiko ena chifukwa choti zipatala zawo zili ndi zipangizo zamakono.

^ ndime 15 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 18 Mfundo yakuti akufa adzauka ikhozanso kuthandiza munthu kuti apeze mtendere wamumtima. Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009 yomwe imafotokoza mfundo za m’Baibulo zosonyeza kuti mwina ana osabadwa amene anamwalira adzaukitsidwa.