Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo za Chiheberi limapezeka kambirimbiri m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Dzina la Mulungu

Dzina la Mulungu

Anthu ambiri amatchula Mulungu ndi maina audindo ngati Ambuye, Wamuyaya, Allah kapena amangoti Mulungu. Komabe Mulungu ali ndi dzina lake lenileni. Koma kodi ndi koyenera kugwiritsa ntchito dzinalo?

Kodi dzina la Mulungu ndi ndani?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

 

Akhristu ambiri amakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi Yesu. Enanso amanena kuti chifukwa chakuti Mulungu Wamphamvuyonse ndi m’modzi yekha, kugwiritsa ntchito dzina lake lenileni n’kosafunika. Anthu enanso amanena kuti kugwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu n’kosayenera.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse. Choncho Yesu si dzina la Mulungu. Yesu anauza anthu kuti azipemphera kuti: “Atate, dzina lanu liyeretsedwe.” (Luka 11:2) Nthawi ina, nayenso anapemphera kwa Mulungu kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.”​Yohane 12:28.

Mulungu anadzitchula yekha m’Baibulo kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense.” (Yesaya 42:8) M’Chichewa, dzina la Mulungu ndi “Yehova” ndipo m’Chiheberi komwe dzinali linachokera, linkalembedwa ndi zilembo 4 zomwe ndi YHWH. M’malemba a Chiheberi dzinali limapezekamo ka 7,000. * Dzinali limapezeka kambirimbiri kuposa maina ngati “Mulungu,” “Wamphamvuyonse,” kapena “Ambuye.” Limapezekanso kwambiri kuposa maina ngati Abulahamu, Mose komanso Davide.

Palibe paliponse m’Baibulo pomwe Mulungu analetsa kugwiritsa ntchito dzina lake moyenera. Malemba amasonyeza kuti atumiki a Mulungu ankagwiritsa ntchito dzina lake momasuka. Dzina la Yehova linkapezekanso m’mayina omwe ankapereka kwa ana awo. Mwachitsanzo dzina lakuti Eliya, limatanthauza kuti Mulungu wanga ndi Yehova. Ndipo dzina lakuti Zekariya, limatanthauza kuti Yehova wandikumbukira. Atumiki a Mulunguwa ankathanso kugwiritsa ntchito dzinali akamacheza ndi anzawo.​—Rute 2:4.

Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito dzina lake. Timalimbikitsidwanso kuti ‘tiziyamika Yehova ndi kuitana pa dzina lake.’ (Salimo 105:1) Yehova amachitanso chidwi ndi anthu amene ‘amaganizira za dzina lake.’​—Malaki 3:16.

“Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18.

Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani?

Akatswiri ena amakhulupirira kuti m’Chiheberi dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu akhoza kudzichititsa kapena kuchititsa zinthu zomwe analenga kukwaniritsa zomwe akufuna. Mulungu Wamphamvuyonse yekha yemwenso ndi Mlengi, ndi amene angakwanitse kuchita zimenezi.

KODI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOTHANDIZA BWANJI?

 

Mukadziwa tanthauzo la dzina la Mulungu, zingakuthandizeni kuti mumudziwe bwino. Sizingakuvuteni kuti mukhale naye pa ubwenzi. Ndipo kodi zingatheke kukhala ndi mnzanu koma osam’dziwa dzina? Mulungu nayenso anatiuza dzina lake n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi.​—Yakobo 4:8.

Sitingakayikire kuti nthawi zonse Mulungu adzakwaniritsa zimene analonjeza chifukwa zimenezo n’zogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani.” (Salimo 9:10) Mudzayamba kukhulupirira kwambiri Yehova mukadziwa kuti dzinali ndi logwirizana ndi makhalidwe ake monga, kukoma mtima kosatha, chifundo, chikondi komanso chilungamo. (Ekisodo 34:5-7) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova adzapitirizabe kukwaniritsa zimene analonjeza ndipo sadzalephera.

Kudziwa tanthauzo la dzina la Mulungu Wamphamvuyonse ndi mwayi waukulu. Zingakuthandizeni kupeza madalitso panopo komanso mtsogolo. Mulungu akulonjeza munthu amene wadziwa dzina lake kuti: “Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.”​—Salimo 91:14.

“Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”​Yoweli 2:32.

Mmene dzina la Mulungu limalembedwera m’zinenero zosiyanasiyana

^ ndime 9 M’mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu ndipo m’malomwake anaikamo dzina laudindo lakuti “AMBUYE” lolembedwa ndi zilembo zazikulu. Pomwe m’mabaibulo ena dzina la Mulungu anangolilemba m’mavesi owerengeka kapena m’mawu a m’munsi okha. Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika dzina la Mulungu limapezeka pafupifupi m’mabuku onse.