Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?

Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?

Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?

“Ndimadziwa kuti aliyense amakhala ndi nkhawa, koma zanga ndiye zawonjeza. Munthune mavuto andichulukira. Mwachitsanzo, nthawi zonse ndimafunika kusamalira mwamuna wanga yemwe sangakwanitse kuchita chilichonse payekha komanso ali ndi vuto la muubongo.”—Jill. *

“Mkazi wanga anandithawa, ndipo ndinkafunika kulera ndekha ana athu awiri. Kuchita zimenezi sikunali kophweka. Kuwonjezera pamenepo, ndinachotsedwa ntchito moti ndinalibe ndalama zokwanira zoti n’kukonzetsera galimoto yanga. Sindinkadziwa choti ndichite moti ndinkada nkhawa kwambiri. Pa nthawiyi ndinaganiza zoti ndingodzipha. Ndinkadziwa kuti kuchita zimenezi n’kulakwa choncho ndinapempha Mulungu kuti andithandize kuthana ndi mavuto angawa.”​—Barry.

Kodi nthawi zina nanunso mumakhala ndi nkhawa ngati mmene zinalili ndi Jill komanso Barry? Ngati ndi choncho, nkhani zotsatirazi zikuthandizani. Nkhanizi zikufotokoza zimene zimachititsa kuti anthu azikhala ndi nkhawa, mmene nkhawa zimakhudzira thanzi lathu komanso zimene tingachite kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambiri.

^ ndime 3 Mayina asinthidwa.