Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi Muli na Nkhawa?

Kodi Muli na Nkhawa?

Jill. a anati: “N’zoona kuti aliyense amakhala na nkhawa, koma ine zanyanya. Si vuto limodzi cabe limene nakumanapo nalo. Nakumana na mavuto osiyana-siyana ambili. Kuwonjezela apo, kwa nthawi yaitali nakhala nikusamalila mwamuna wanga amene amadwala maganizo komanso matenda ena ake.”

Barry anati: “Mkazi wanga ananithaŵa, ndipo n’nali kulela nekha ana aŵili. Kulela nekha ana kunali kovuta. Kuwonjezela apo, nchito inasila, ndipo sin’nali kukwanitsa kupeza ndalama zokonzetsela motoka. N’nasoŵa cocita. Kukamba zoona, n’nali na nkhawa kwambili. N’nali kudziŵa kuti kudzipha n’kulakwa, conco n’napempha Mulungu kuti nife cabe.”

Mofanana ndi Jill na Barry, kodi nthawi zina nkhawa zimakuculukilani? Ngati n’conco, lekani kuti nkhani zokonkhapo zikutonthozeni na kukuthandizani. Nkhanizi zidzafotokoza zinthu zimene kaŵili-kaŵili zimabweletsa nkhawa, mmene nkhawa zingatikhudzile, komanso zimene tingacite kuti ticepetse nkhawa.

a Maina ena asinthidwa.