Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?

Zomwe Zimachititsa Kuti Anthu Azikhala ndi Nkhawa

Zomwe Zimachititsa Kuti Anthu Azikhala ndi Nkhawa

Akatswiri a pachipatala china chotchuka, chotchedwa Mayo, anati: “Nthawi zambiri anthu akuluakulu ndi amene akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Zimenezi zili chonchi chifukwa moyo wa masiku ano umasinthasintha komanso ndi wosadalirika.” Zina mwa zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azikhala ndi nkhawa ndi monga:

  • kutha kwa banja

  • kumwalira kwa munthu amene timamukonda

  • matenda aakulu

  • ngozi yaikulu

  • kuphwanya malamulo

  • kukhala wotanganidwa nthawi zonse

  • ngozi zachilengedwe kapena zochititsidwa ndi anthu

  • kupanikizika ndi zochitika za kuntchito kapena kusukulu

  • kusowa kwa ntchito komanso mavuto a zachuma