Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?

Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?

Acipatala cochuka cochedwa Mayo Clinic anati: “Nkhawa zikuwonjeka kwa anthu akulu-akulu ambili. Umoyo m’dzikoli ni wosadalilika, ndipo zinthu zingasinthe nthawi iliyonse.” Onani zina mwa zinthu zimene zimabweletsa nkhawa:

  • kusila kwa cikwati

  • imfa ya munthu wokondedwa

  • matenda aakulu

  • ngozi yaikulu

  • upandu

  • umoyo wokhala na zocita zambili

  • matsoka acilengedwe komanso ocititsidwa ndi anthu

  • kupanikizika na sukulu komanso nchito

  • nkhawa zokhudza nchito, na kusoŵa ndalama