Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

5 Kodi Kuvutika Kudzatha?

5 Kodi Kuvutika Kudzatha?

Chifukwa Chake Kudziwa Yankho la Funsoli Kuli Kofunika

Ngati patakhala chifukwa chokhulupirira kuti kuvutika kudzatha, ndiye kuti tikhoza kuyamba kuona kuti moyo wathu uli ndi cholinga, komanso tikhoza kuyamba kukonda kwambiri Mulungu.

Taganizirani Izi

Anthu ambiri angakonde atathetsa mavuto onse, koma alibe mphamvu zokwanira zochitira zimenezi. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

Ngakhale kuti luso lopanga mankhwala lakula kwambiri . . .

  • Matenda a mtima adakali nthenda imene ikupha anthu kwambiri.

  • Khansa imapha anthu mamiliyoni chaka chilichonse.

  • Dr.  David Bloom analemba kuti, “Anthu masiku ano akudwala matenda amene akhalapo kwa nthawi yaitali, amene ndi achilendo, komanso ena amene tinkaganiza ngati anatha.”—Frontiers in Immunology.

Ngakhale kuti mayiko ena ndi olemera . . .

  • Chaka chilichonse, ana mamiliyoni ambiri amafa ndipo ambiri mwa anawa ndi a m’mayiko osauka.

  • Anthu mabiliyoni ambiri akukhala popanda zinthu zokwanira zowathandiza kuti azikhala moyo waukhondo.

  • Anthu mamiliyoni mahandiredi ambiri sangathe kupeza madzi abwino.

Ngakhale kuti anthu ambiri akudziwa bwino zokhudza maufulu a anthu . . .

  • Bizinezi yogulitsa anthu ikuchitikabe m’mayiko ambiri ndipo pali mayiko ena omwe sanaimbepo mlandu anthu amene amachita zimenezi. Zili choncho chifukwa “boma silidziwa kuti zikuchitika, kapena limadziwa ndithu, koma lilibe zinthu zolithandiza kugwira anthuwa n’kuwaimba mlandu.”​—Lipoti la United Nations.

    KUTI MUDZIWE ZAMBIRI

    Onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? pa jw.org.

Zimene Baibulo Limanena

Mulungu amatiganizira.

Amadziwa tikamavutika komanso tikakhala ndi chisoni.

“[Mulungu] sananyoze, kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa. Ndipo sanam’bisire nkhope yake. Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.”SALIMO 22:24.

“Pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”​1 PETULO 5:7.

Sitidzavutika mpaka kalekale.

Baibulo limatilonjeza kuti cholinga cha Mulungu polenga anthufe chidzakwaniritsidwa.

“Mulungu . . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.

Mulungu adzathetsa zimene zimachititsa kuti anthu azivutika.

Iye adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake.

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, . . . ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”​DANIELI 2:44.