Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Moyo Wosangalala

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Moyo Wosangalala

“Ngakhale kuti nthawi zina ndimakhumudwa ndi zinthu zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli monga nkhondo, umphawi, matenda komanso kuchitiridwa nkhanza kwa ana, ndili ndi chiyembekezo kuti zimenezi zidzatha.”​—RANI. *

Rani anapeza chimwemwe chenicheni ataphunzira kuti Mlengi wathu, yemwe ndi Mulungu wamphamvuyonse, ndi amene amapereka nzeru zothandiza. Mukamawerenga mfundo zotsatirazi, onani mmene mfundo zomwe Mulungu akutiphunzitsa zingakuthandizireni kuti . . .

  • mukhale ndi banja losangalala

  • muzikhala mwamtendere ndi anthu ena

  • muzikhala okhutira

  • mudziwe chomwe chimachititsa kuti tizivutika komanso kufa

  • mukhale ndi chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo

  • mumudziwe bwino Mlengi wathu komanso mukhale mnzake

Muonanso kuti Mlengi wathu samangopereka nzeru kwa anthu ochepa, koma amazipereka kwa wina aliyense amene amazifunafuna.

^ ndime 2 Mayina asinthidwa m’magaziniyi.