Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira

Tonsefe, kaya tili pabanja kapena ayi, ana kapena achikulire, timafuna kukhala osangalala komanso okhutira. Mlengi wathu amafunanso kuti tizikhala choncho, ndipo amatipatsa malangizo abwino kwambiri.

Tizigwira Ntchito Mwakhama

“Agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”—AEFESO 4:28.

Mlengi wathu amatilimbikitsa kuti tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Chifukwa chiyani? Munthu amene amagwira ntchito molimbika amakhala wosangalala chifukwa amapeza zinthu zofunika pa moyo wake komanso wa banja lake. Angathenso kuthandiza ena amene akufunika thandizo, ndipo amakhalanso wodalirika kwa abwana ake. Choncho munthu amene amagwira bwino ntchito, amakhalitsa pantchitopo. Malemba amafotokoza momveka bwino kuti zotsatirapo za kugwira ntchito mwakhama “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”​—Mlaliki 3:13.

Tizikhala Oona Mtima

“Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—AHEBERI 13:18.

Tikakhala oona mtima anthu ena amatilemekeza, timakhala ndi mtendere wamumtima, timagona tulo tabwino komanso anthu ena amatidalira. Koma anthu achinyengo amadzilanda okha zinthu zimenezi komanso chikumbumtima chawo chimawavutitsa ndipo amakhala mwamantha kuti tsiku lina akhoza kudzagwidwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

Muziona Ndalama Moyenera

“Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”​—AHEBERI 13:5.

Timafunika ndalama kuti tigule chakudya ndi zinthu zina zofunikira. Komabe, “kukonda ndalama” n’koopsa kwambiri. Kungachititse munthu kuti azigwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zambiri kuti azifunafuna ndalama zochuluka. Chifukwa chakuti amangosakasaka ndalama kwambiri, banja lake silingamayende bwino, sangamakhale ndi nthawi yocheza ndi ana ake komanso zingakhudze thanzi lake. (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndiponso munthu amene amakonda ndalama akhoza kuyesedwa kuti achite zinthu zachinyengo. Munthu wina wanzeru anati: “Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri, koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.”​—Miyambo 28:20.

Sankhani Maphunziro Abwino Kwambiri

“Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”​—MIYAMBO 3:21.

Maphunziro abwino amatithandiza kukhala anthu odalirika. Koma maphunziro am’dzikoli paokha sangatithandize kukhala otetezeka komanso osangalala. Kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu, timafunika maphunziro amene Yehova amatipatsa. Malemba amanena kuti munthu amene amamvera Mulungu, “zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​—Salimo 1:1-3.