Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu ndi Anthu Ena?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu ndi Anthu Ena?

Anthu akhoza kulumikizana mosavuta ngakhale atakhala m’mayiko otalikirana kwambiri chifukwa cha kutumizirana mameseji pa foni, maimelo, kulankhulana pa vidiyokomfelensi komanso kucheza pamalo ochezera a pa intaneti. Zipangizo zamakono zimawathandiza kwambiri.

Komabe, anthu amene amakonda kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono pofuna kucheza ndi anzawo, nthawi zina . . .

  • amalephera kumvetsa mmene anzawo akumvera.

  • amadzimva kuti ali okhaokha komanso amasowa ocheza naye.

  • amaganizira zofuna zawo zokha kuposa za ena.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

CHIFUNDO

Kuti tithe kusonyeza ena chifundo timafunika kuganizira mmene akumvera zomwe zimafuna kudekha komanso kuleza mtima. Zimenezi sizingatheke ngati tatanganidwa kuwerenga komanso kutumiza mameseji, kapena kuona zithunzi pamalo ochezera a pa intaneti.

Ngati zipangizo zamakono zikukulamulirani, kuyankha mameseji a anzanu kukhoza kukhala mtolo wokulemetsani. M’malo mofuna kuthandiza mnzanu amene akufunikiradi thandizo, cholinga chanu chimangokhala kuona komanso kuyankha mofulumira mamesejiwo.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mungasonyeze bwanji kuti ‘mumamvera ena chisoni’ mukamagwiritsa ntchito zipangizo zamakono pocheza ndi anzanu?​—1 PETULO 3:8.

KUSOWA OCHEZA NAYE

Kafukufuku wina anapeza kuti, pambuyo poti aona zinthu zina ndi zina pamalo ochezera a pa intaneti, anthu ambiri amadzimva kuti ndi osafunika. Ochita kafukufukuyu ananena kuti kuona zithunzi kapena zinthu zina zimene anthu ena aika kungachititse munthu kudziona kuti “palibe chilichonse chanzeru chimene wachita.”

Komanso kuona zithunzi zosangalatsa zimene ena aika, kungachititse munthu kuyamba kudziyerekezera molakwika ndi anthu ena. Ndipotu zimaoneka ngati aliyense akusangalala ndi moyo, pomwe inuyo simukusangalala.

ZOTI MUGANIZIRE: Mukamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mungatani kuti musamadziyerekezere molakwika ndi anthu ena?​—AGALATIYA 6:4.

KUDZIGANIZIRA TOKHA

Mphunzitsi wina analemba kuti ana ena a m’kalasi mwake anali odzikonda, ndipo ankangofuna kukhala ndi anzawo omwe “angawachitire zinazake.” * Anthu oterewo amangoganizira zimene angapeze kwa anzawowo. Anthu amenewa amaona anzawo ngati foni imene akhoza kungoigwiritsa ntchito akaifuna kenako n’kuizimitsa.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi zimene mumaika pa intaneti, zimasonyeza kuti muli ndi chizolowezi cha mpikisano kapena chomangoganizira za inu nokha?—AGALATIYA 5:26.

ZIMENE MUNGACHITE

GANIZIRANI MMENE MUMAGWIRITSIRA NTCHITO ZIPANGIZO ZAMAKONO

Ngati zipangizo zamakono sizimakulamulirani koma inuyo ndi amene mumazilamulira, zingakuthandizeni kuti mukhale ndi anzanu abwino komanso kuti mukhale nawo pa ubwenzi wolimba.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”​—1 AKORINTO 13:4, 5.

Pa mfundo zotsatirazi sankhani zimene mungakonde kuti mugwiritse ntchito kapena lembani zanu zimene mungaganize.

  • Muzicheza ndi anthu pamasom’pamaso (kusiyana n’kumangolemberana mameseji kapena maimelo)

  • Mukamacheza ndi anthu ena muziika patali foni yanu kapena muziika ku sailenti

  • Chepetsani nthawi imene mumakhala mukuona zinthu zimene anthu aika pamalo ochezera a pa intaneti

  • Muzimvetsera ena akamalankhula

  • Muziimbira foni mnzanu amene akukumana ndi mavuto

^ ndime 17 Zili m’buku lakuti Reclaiming Conversation.