Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu na Ena?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu na Ena?

Masiku ano, ngakhale anthu amene amakhala m’maiko otalikilana kwambili, angakwanitse kukambilana mosavuta poseŵenzetsa zipangizo zamakono. Angacite izi mwa kutumizilana mameseji, kukambilana pa vidiyokomfalensi, na kuceza pa tsamba la intaneti. Kwa iwo, zipangizo zamakono n’zothandiza kwambili.

Komabe, anthu amene amakonda kwambili kuseŵenzetsa zipangizo zamakono pokambilana na anzawo, nthawi zambili . . .

  • saonetsa cifundo kweni-kweni kwa anzawo.

  • amakhala osungulumwa komanso opsinjika maganizo.

  • amaganizila kwambili za iwo eni.

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

CIFUNDO

Kuti tionetse cifundo kwa munthu wina, tiyenela kukhala na nthawi yomuganizila munthuyo. Kucita zimenezi kungakhale kovuta ngati tili na mameseji ambili ofunika kuŵelenga kapena kutumiza, komanso ngati tili na zinthu zambili zoyenela kuona pa tsamba la mcezo la pa intaneti.

Ngati zipangizo zamakono zimakulamulilani, m’kupita kwa nthawi mungayambe kuona kuti kuyankha mameseji amene anzanu amakulembelani ni cinchito cacikulu. Ndipo mumakhala na colinga congoyankha mameseji onse mwamsanga kuti athe, m’malo mothandiza mnzanu amene akufunikila thandizo.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Mukamatumiza mameseji kwa anzanu pa foni kapena pa zipangizo zina, mungaonetse bwanji kuti ‘mumawamvela cisoni’?—1 PETULO 3:8.

KUSUNGULUMWA NA KUPSINJIKA MAGANIZO

Akatswili ena a sayansi atafufuza, anapeza kuti anthu ambili amakhala osasangalala pambuyo poseŵenzetsa tsamba linalake lochuka la mcezo la pa intaneti. Akatswiliwo anakamba kuti kuyang’ana mapikica na zinthu zina zimene ena aika pa intaneti kungapangitse munthu “kuona kuti sanacite ciliconse copindulitsa.”

Kuwonjezela apo, kuona zithunzi zabwino zimene ena aika pa intaneti, kungapangitse kuti muyambe kudziyelekezela na ena molakwika. Izi zili conco cifukwa pa masamba a mcezo a pa intaneti, anthu amaoneka monga amakhala osangalala nthawi zonse. Koma ife tingamaone monga kuti umoyo wathu ni wosasangalatsa.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Mukamaseŵenzetsa masamba a mcezo a pa intaneti, kodi mungacite ciani kuti mupewe kudziyelekezela molakwika na anthu ena?—AGALATIYA 6:4.

KUGANIZILA KWAMBILI ZA INU MWINI

Mphunzitsi wina anakamba kuti ana a sukulu ena m’kalasi yake, amakonda kugwilizana na anthu okhawo amene amaona kuti “angawacitile zinazake zabwino.” * Anthu otelo amangoganizila phindu limene angapeze kwa mabwenzi awo. Ndipo angayambe kuona mabwenzi awo monga zipangizo zimene angaziseŵenzetse kapena kuzizima pamene afunila.

ZOYENELA KUZIGANIZILA: Kodi zimene mumaika pa intaneti zimaonetsa kuti muli na mtima wampikisano kapena mumakonda kuganizila za inu mwini?—AGALATIYA 5:26.

ZIMENE MUNGACITE

PENDANI MMENE MUMASEŴENZETSELA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Kugwilitsila nchito bwino zipangizo zamakono, kudzakuthandizani pokambilana na mabwenzi anu na kulimbitsa ubwenziwo.

MFUNDO YA M’BAIBO: “Cikondi . . . sicisamala zofuna zake zokha.”—1 AKORINTO 13:4, 5.

Sankhani malingalilo amene mungakonde kuwaseŵenzetsa, kapena lembani malingalilo anu.

  • Muzikonda kukambilana mwacindunji na anthu (m’malo mowatumila cabe mameseji pa foni kapena pa zipangizo zina)

  • Pamene mukambilana na anthu ena, ikani patali foni (kapena iikeni pa sailensi)

  • Cepetsani nthawi imene mumathela poyang’ana zinthu zimene ena amaika pa masamba a mcezo a pa intaneti

  • Muzimvetsela mosamala ena akamakamba nanu

  • Tumilani foni mnzanu amene akukumana na vuto linalake

^ ndime 17 Zimenezi zinafotokozedwa m’buku lakuti Reclaiming Conversation.