Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

DZIKOLI LILI PA MAVUTO AAKULU

3 | Tetezani Ubale Wanu na Ena

3 | Tetezani Ubale Wanu na Ena

CIFUKWA CAKE KUCITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Pamene nkhawa ikula cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, mosadziŵa anthu ambili amalola ubale wawo na anthu ena kusokonezeka.

  • Anthu amadzipatula kwa mabwenzi awo.

  • Anthu okwatilana amangokangana-kangana.

  • Makolo sakhala na cidwi kwenikweni cofuna kudziŵa nkhawa za ana awo.

Zimene Muyenela Kudziŵa

  • Mabwenzi ni ofunika kwambili cifukwa amatithandiza kukhala na thanzi labwino, komanso kukhala olimba makamaka tikakumana na mavuto.

  • Nkhawa yobwela cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, ingakhudze kwambili umoyo wa banja lanu.

  • Ana akamva kapena kuona zinthu zoopsa pa nyuzi, angacite mantha kwambili kuposa mmene mungaganizile.

Zimene Mungacite Pali Pano

Baibo imati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

Mabwenzi angatithandize na kutipatsa ulangizi wabwino. Kungodziŵa kuti munthu wina wake amasamala za ife kungatithandize kuti tipilile mavuto a tsiku na tsiku.