Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo

Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo

IRI ndi bukhu la nkhani zeni-zeni. Zatengedwa m’bukhu lalikulu koposa, Baibulo. Nkhani’zo zimakulongosolerani mbiri kuyambira pamene Mulungu anayamba kulenga kufikira lero lino. Zimanena’nso za zimene Mulungu akulonjeza kuchita m’tsogolo.

Bukhu’li limakupatsani lingaliro la zimene Baibulo limazinena. Limasimba za anthu a m’Baibulo ndi zinthu zimene iwo anachita. Limasonyeza’nso chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wosatha m’dziko lapansi laparadaiso chimene Mulungu wapatsa anthu.

Muli nkhani 116 m’bukhu’li. Zimene’zi zaikidwa m’zigawo zisanu ndi zitatu. Tsamba limodzi poyambirira pa chigawo chiri chonse limalongosola mwachidule zimene ziri m’chigawo’cho. Nkhani’zo ziri molingana ndi m’mene zochitika zinachitikira m’mbiri. Zimene’zi zimakuthandizani kuphunzira nthawi, mogwirizana ndi zochitika zina, imene zochitika zinachitika m’mbiri.

Nkhani’zo zikusimbidwa mosabvuta. Ambiri a ana ang’ononu mudzakhoza kudziwerengera nokha. Makolonu mudzaona kuti tiana tanu tidzakondwera kutiwerengera nkhani’zi mobwereza-bwereza. Mudzaona kuti bukhu’li liri n’zokondweretsa zambiri kwa ana ndi akulu omwe.

Malemba a Baibulo akuperekedwa pa mapeto a nkhani iri yonse. Mukulimbikitsidwa kuwerenga zigawo za Baibulo’zi pa zimene nkhani’zo zazikidwapo. Mukamaliza kuwerenga nkhani iliyonse, yesani kuyankha mafunso a nkhaniyo amene akupezeka kumapeto kwa nkhani nambala 116.