Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 1

Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu

Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu

ZINTHU zabwino zimene tiri nazo zachokera kwa Mulungu. Iye anapanga dzuwa lidziunikira masana, ndi mwezi ndi nyenyezi kuti tikhale ndi kuunika usiku. Ndipo Mulungu anapanga dziko lapansi kuti tikhalepo.

Koma dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi dziko lapansi sizinali zoyamba kupangidwa ndi Mulungu. Kodi mukudziwa choyamba? Mulungu anayamba kupanga anthu onga iye. Sitingaone anthu’wa, monga momwe sitingaonere Mulungu. M’Baibulo amene’wa amachedwa angelo. Mulungu anapanga angelo kukhala naye kumwamba.

Mngelo woyamba kupangidwa ndi Mulungu anali wapadera kwambiri. Ndiye Mwana woyamba wa Mulungu, ndipo anagwira ntchito ndi Atate wake. Anathandiza Mulungu kupanga dzuwa, mwezi, nyenyezi ndipo’nso dziko lathu lapansi.

Kodi dziko lapansi linali lotani pa nthawi’yo? Poyamba palibe akanakhala pa dziko lapansi. Panalibe kanthu kusiyapo chinyanja pa mtunda wonse. Koma Mulungu anafuna kuti anthu akhalepo. Chotero anayamba kutikonzera zinthu. Kodi anachitanji?

Eya, choyamba dziko’lo linafunikira kuunika. Chotero Mulungu anachititsa kuunika kuchokera ku dzuwa kuwalira dziko. Anapanga kuti pakhale usiku ndi usana. Kenako Mulungu anapangitsa mtunda kutundumuka pa madzi a nyanja’wo.

Poyamba panalibe kanthu pa mtundapo. Panali ngati chithunzi mukuona apa’chi. Panalibe maluwa, mitengo kapena zinyama. Munalibe ngakhale nsomba m’nyanjamo. Mulungu anali ndi ntchito yoti achite yochuluka kupanga dziko lapansi labwino’di kwa zinyama ndi anthu kukhalapo.