Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 1

Mulungu Ayamba Kupanga Vinthu

Mulungu Ayamba Kupanga Vinthu

VINTHU vonse vabwino vimene tili navo vimacokela kwa Mulungu. Iye anapanga dzuŵa kuti liziwala usana, ndipo anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti ziziunikila usiku. Ndiponso Mulungu anapanga dziko lapansi kuti ife tizikhalapo.

Koma dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi dziko lapansi sivinali vinthu voyambilila vimene Mulungu anapanga. Kodi udziŵa cinthu coyamba cimene Mulungu anapanga? Coyamba Mulungu anapanga anthu ofanana naye. Anthu amenewa sitingawaone monga mmene sitingaonele Mulungu. Mu Baibo anthu amenewa amachedwa angelo. Mulungu anapanga angelo kuti azikhala naye kumwamba.

Mngelo woyamba amene Mulungu anapanga anali wapadela kwambili. Anali Mwana woyamba wa Mulungu, ndipo anali kugwila nchito ndi Atate ake. Anathandiza Mulungu kupanga vinthu vonse. Anathandiza kupanga dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi dziko lathu lapansi.

Kodi dziko lapansi panthawi imeneyo linali bwanji? Paciyambi palibe amene anali kukhala padziko lapansi. Panalibe ciliconse. Koma dziko lonse linali nyanja ikulu kwambili. Koma Mulungu anali kufuna kuti anthu akhale padziko lapansi. Conco anayamba kutikonzela zinthu. Kodi anacita ciani?

Coyamba, padziko lapansi panali kufunikila kuwala. Conco Mulungu anapanga dzuŵa kuti liziwala padziko lapansi. Analipanga kuti pazikhala usana ndi usiku. Pambuyo pake, Mulungu anacititsa kuti nthaka inyamuke kucokela pansi pa nyanja.

Poyamba, panthaka panalibe ciliconse. Panali kuoneka monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Panalibe maluŵa, mitengo, kapena vinyama. Mu nyanja munalibe ngakhale nsomba zilizonse. Mulungu anali ndi nchito ina ikulu yopanga dziko lapansi kukhala malo abwino kwambili, akuti anthu na vinyama azikhalapo.

Yeremiya 10:12; Akolose 1:15-17; Genesis 1:1-10.