Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 6

Mwana Wabwino, Ndi Mwana Woipa

Mwana Wabwino, Ndi Mwana Woipa

TSOPANO ona mmene Kaini ndi Abele aonekela. Onse akula. Kaini ni mlimi. Amalima za m’munda monga tiligu, zipatso ndi ndiwo zamasamba.

Koma Abele amaweta nkhosa kapena kuti mbelele. Amakonda kusamalila tuŵana twa nkhosa. Tumakula kukhala nkhosa zikulu-zikulu, cakuti Abele akhala ndi nkhosa zambili zimene amasamalila.

Tsiku lina Kaini ndi Abele akonza nsembe zakuti apeleke kwa Mulungu. Kaini abweletsa zakudya za kumunda kwake. Koma Abele abweletsa nkhosa yonenepa bwino kwambili. Yehova akondwela kwambili ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sakondwela ndi Kaini ndi nsembe yake. Kodi udziŵa cifukwa cake sanakondwele?

Si cifukwa cabe cakuti nsembe ya Abele ni yabwino kupambana ya Kaini. Koma cifukwa cacikulu n’cakuti Abele ni munthu wabwino. Iye akonda Yehova ndi mkulu wake Kaini. Koma Kaini ni munthu woipa, ndipo sakonda mng’ono wake Abele.

Pa cifukwa cimeneci, Mulungu auza Kaini kuti asinthe macitidwe ake. Koma Kaini safuna kumvela. Iye ni wokalipa kwambili cifukwa cakuti Mulungu amakonda Abele kupambana iye. Conco Kaini auza Abele kuti, ‘Tiye kumunda.’ Pamene ali kumunda kuja aŵili cabe, Kaini amenya mng’ono wake Abele. Wam’menya mwamphamvu kwambili cakuti wamupha. Cimene kaini wacita ni cinthu coipa kwambili, si conco?

Ngakhale kuti Abele anafa, Mulungu akali kumukumbukila. Abele anali munthu wabwino, ndipo Yehova samaiŵala anthu abwino. Conco, tsiku lina Yehova Mulungu adzaukitsa Abele kuti akakhalenso ndi moyo. Panthawi imeneyo Abele sadzafanso. Koma adzakhala ndi moyo wamuyaya pano padziko lapansi. Kodi ufuna kuti ukadziŵane ndi anthu monga Abele?

Koma Mulungu sakondwela ndi anthu ali monga Kaini. Ndiye cifukwa cake pamene Kaini anapha m’bale wake, Mulungu anam’patsa cilango mwa kum’pilikitsila kumalo akutali kwambili kucoka kwa acibanja ake onse. Pamene Kaini anayenda kukakhala kumalo ena a dziko lapansi, anatenga mmodzi wa alongosi ake, ndipo anakhala mkazi wake.

M’kupita kwa nthawi, Kaini ndi mkazi wake ameneyo anayamba kubala ana. Adamu ndi Hava anabalanso ana ena amuna ndi akazi. Pamene anao anakula, nao anakwatila ndi kukwatiwa ndi kubala ana ao. Posapita nthawi, padziko lapansi panakhala anthu ambili. Tiye tiphunzile za ena mwa anthu amenewo.

Genesis 4:2-26; 1 Yohane 3:11, 12; Yohane 11:25.