Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 9

Nowa Apanga Cingalawa

Nowa Apanga Cingalawa

NOWA anali ndi mkazi ndi ana amuna atatu. Maina a ana ake anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Ndipo mwana aliyense anali ndi mkazi wake. Conco, anthu onse m’banja la Nowa analimo 8.

Tsopano Mulungu anauza Nowa kucita cimene sanacitepo. Anamuuza kuti apange cingalawa cacikulu. Cingalawa cimeneci cinali monga ciboti cikulu, koma cinali kuoneka monga cibokosi cacikulu ndi cacitali kwambili. Mulungu anamuuza kuti cikhale cosanjikiza katatu, pansi, pakati ndi pamwamba. Ndipo anati aikemo zipinda. Zipinda zina zinali za Nowa ndi banja lake, zina zinali za zinyama, ndipo zina zinali zoikamo zakudya ndi zinthu zina.

Mulungu anauzanso Nowa kuti acimate bwino-bwino cingalawaco kuti madzi asamaloŵe. Mulungu anakamba kuti: ‘Ndidzabweletsa cigumula ca madzi padziko lapansi kuti ciononge camoyo ciliconse ca pansi pa thambo. Ndipo aliyense amene sali m’cingalawa adzafa.’

Nowa ndi ana ake anamvela Yehova, ndipo anayamba kupanga ciboti cija. Koma anthu ena anali kuŵaseka. Ndipo anapitiliza kukhala anthu oipa. Palibe amene anakhulupilila Nowa pamene anawauza zimene Mulungu anali kudzacita.

Panapita zaka zambili kuti atsilize kumanga cingalawa, cifukwa cinali cacikulu kwambili. Tsopano pamene anatsiliza, Mulungu anauza Nowa kuti angenetse vinyama m’cingalawa muja. Mulungu anamuuza kuti angenetse nyama ziŵili-ziŵili, imuna ndi ikazi. Koma Mulungu anauza Nowa kuti mitundu ina ya zinyama angenetse zisanu ndi ziŵili. Mulungu anauzanso Nowa kuti aloŵetse mitundu yonse ya mbalame. Nowa anacita zimene Mulungu anamuuza.

Pambuyo pake, Nowa ndi banja lake naonso analoŵa m’cingalawa. Ndiyeno Mulungu anatseka citseko. Pamene anali mkati, Nowa ndi banja lake anayembekezela. Ganizila cabe kuti uli nao m’cingalawa muja, uyembekezela. Kodi cigumula cidzacitikadi, monga mmene Mulungu anakambila?

Genesis 6:9-22; 7:1-9.