Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 11

Utawaleza Woyamba

Utawaleza Woyamba

KODI udziŵa cinthu coyamba cimene Nowa anacita pamene iye ndi banja lake anacoka m’cingalawa? Anapeleka nsembe kapena kuti mphatso kwa Mulungu. Ona mmene iye acitila zimenezi pacithunzi-thunzi apa. Nowa anapeleka nyama zimenezi monga mphatso kuti aonge zikomo kwa Mulungu cifukwa copulumutsa banja lake pa cigumula.

Kodi uganiza kuti Yehova analandila nsembe imeneyi? Inde, anailandila. Conco, analonjeza Nowa kuti sadzaononganso dziko ndi Cigumula.

Patapita kanthawi, madzi onse anauma, ndipo Nowa ndi banja lake anatuluka m’cingalawa ndi kuyamba moyo watsopano. Mulungu anawadalitsa ndipo anawauza kuti: ‘Mubalane, muculuke mudzaze dziko lapansi.’

Koma m’kupita kwa nthawi, anthu akanamvela za cigumula, akanacita mantha kuti cigumula cingacitikenso. Conco Mulungu anapatsa anthu cinthu cina cowakumbutsa lonjezo lakuti sadzaononganso dziko lonse lapansi ndi cigumula. Kodi udziŵa cimene anawapatsa? Unali utawaleza.

Nthawi zambili, utawaleza umaonekela kumwamba dzuŵa likaŵala, mvula ikaleka kugwa. Utawaleza uli ndi makhala kapena kuti mitundu yambili yokongola. Kodi unauonapo utawaleza? Kodi wauona pa cithunzi-thunzi apa?

Mulungu anakamba kuti: ‘Nilonjeza kuti sinidzabweletsanso cigumula coononga anthu ndi nyama. Ndiika utawaleza mu mitambo, ndipo ukaonekela, ndizikumbukila lonjezo langa limeneli.’

Conco, kodi ukaona utawaleza, uyenela kukukumbutsa ciani? Uyenela kukukumbutsa lonjezo la Mulungu lakuti sadzaononganso dziko ndi Cigumula camadzi.

Genesis 8:18-22; 9:9-17.