Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 12

Anthu Amanga Chinsanja

Anthu Amanga Chinsanja

ZAKA zambiri zinapitapo. Ana a Nowa anali ndi ana Ochuluka. Ana ao anakula nakhala ndi ana ochuluka. Posapita nthawi panali anthu ochuluka pa dziko lapansi.

Mmodzi wa amene’wa anali chidzukulu cha Nowa chochedwa Nimrode. Iye anali woipa amene anasaka ndi kupha nyama ndi anthu omwe. Nimrode anadzipanga’nso kukhala mfumu kulamulira pa anthu ena. Mulungu sanakonde Nimrode.

Anthu onse pa nthawi’yo analankhula chinenero chimodzi. Nimrode anafuna kuwasonkhanitsa pamodzi kuti adziwalamulira. Chotero kodi mukudziwa chimene anachita? Anauza anthu’wo kumanga mzinda ndi chinsanja. Mukuwaona m’chithunzi’cho akuumba njerwa.

Yehova sanali wokondwa ndi kumanga’ku. Iye anafuna kuti anthu abalalike ndi kukhala pa dziko lonse lapansi. Koma anthu’wo anati: ‘Tiyeni! timange mzinda ndi nsanja yaitali kwambiri yoti nsonga yake idzafike kumwamba. Pompo tidzadzipangira dzina! Anthu’wo anadzifunira ulemu, osati Mulungu.

Chotero Mulungu analetsa anthu’wo kumanga nsanja. Kodi mukudziwa kuti anakuchita motani? Mwa kulankhulitsa anthu zinenero zosiyana mwadzidzidzi. Omanga’wo sanamvane’nso. Ndicho chifukwa chake mzinda’wo unachedwa Ba’bele. kapena Babulo, kutanthauza ”Chisokonezo.”

Anthu’wo tsopano anayamba kubalalika pa Ba’bele. Timagulu timene tinalankhula chinenero chimodzi tinamkera limodzi ku mbali ina ya dziko lapansi.