Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 13

Abulahamu—mnzake Wa Mulungu

Abulahamu—mnzake Wa Mulungu

MALO ena kumene anthu anayenda kukakhala pamene Cigumula cinatha kunali ku Uri. Malo amenewa anakhala mzinda wofunika kwambili umene unali ndi nyumba zabwino. Koma anthu a kumeneko anali kulambila milungu yonama. Izi n’zimene anthu a ku Babele naonso anali kucita. Anthu ku Uri ndi ku Babele anali osiyana ndi Nowa ndi mwana wake Shemu, amene anapitiliza kutumikila Yehova.

Potsilizila pake, Nowa anamwalila patapita zaka 350, kucokela pamene cigumula cinacitika. Pamene Nowa anamwalila panangopita zaka ziŵili, ndipo mwamuna amene uona pacithunzi-thunzi apa anabadwa. Anali munthu wapadela kwambili kwa Mulungu, dzina lake anali Abulahamu. Iye anali kukhala ndi banja lake mu mzinda wa Uri.

Tsiku lina Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Coka mu dziko lako, pakati pa abale ako, ndipo uyende kudziko limene n’dzakuonetsa.’ Kodi Abulahamu anamvela Mulungu ndi kusiya umoyo wabwino umene anali nao ku Uri? Inde, anamvela Mulungu. Cifukwa cakuti Abulahamu anali kumvela Mulungu nthawi zonse, anachedwa mnzake wa Mulungu.

Ena mwa acibanja a Abulahamu anapita naye pamodzi pamene anacoka ku Uri. Atate ake a Tera ndi mlisa wake Loti anapita naye. N’zoonekelatu kuti Sara, mkazi wa Abulahamu anapita naye pamodzi. M’kupita kwa nthawi onse anafika ku malo ochedwa Harana, kumene Tera anafela. Iwo anali kutali kwambili ndi mzinda wa Uri.

Patapita nthawi yocepa, Abulahamu ndi apabanja lake anacoka ku Harana ndipo anapita kumalo ochedwa Kanani. Ali kumeneko, Yehova anati: ‘N’dzapeleka dziko ili kwa ana ako.’ Abulahamu anakhala ku Kanani ndipo anayamba kukhala mu matenti.

Mulungu anayamba kuthandiza Abulahamu, cakuti anakhala ndi nkhosa ndi ziŵeto zina zambili, ndiponso anali ndi anchito ambili. Koma iye ndi Sara analibe mwana wao-wao.

Pamene Abulahamu anakwanitsa zaka 99, Yehova anati: ‘Ine nicita pangano ndi iwe, ndipo udzakhala tate wa mitundu yambili.’ Koma kodi Abulahamu ndi Sara akanakhala bwanji ndi mwana popeza anali okalamba kwambili?

Genesis 11:27-32; 12:1-7; 17:1-8, 15-17; 18:9-19.