Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 14

Mulungu Ayesa Cikhulupililo Ca Abulahamu

Mulungu Ayesa Cikhulupililo Ca Abulahamu

KODI waona zimene Abulahamu acita pacithunzi-thunzi apa? Ali ndi mpeni kapena kuti naifi, ndipo zioneka kuti afuna kupha mwana wake. N’cifukwa ciani afuna kucita zimenezi? Coyamba, tiye tione mmene Abulahamu ndi Sara anakhalila ndi mwana ameneyu.

Kumbukila kuti Mulungu anawalonjeza kuti adzabala mwana. Koma zimenezi zinali kuoneka kuti sizingacitike, cifukwa Abulahamu ndi Sara anali okalamba kwambili. Komabe, Abulahamu anakhulupilila kuti Mulungu angacite zimene zinali kuoneka kuti ni zosatheka. Conco, n’ciani cimene cinacitika?

Panapita caka cimodzi kucokela pamene Mulungu anawalonjeza. Ndiyeno, pamene Abulahamu anali ndi zaka 100, ndipo Sara zaka 90, io anabala mwana mwamuna, dzina lake Isaki. Mulungu anakwanilitsa zimene anawalonjeza.

Koma pamene Isaki anakula, Yehova anayesa cikhulupililo ca Abulahamu. Anamuitana kuti: ‘Abulahamu!’ Ndipo iye anayankha kuti: ‘Ine mbuyanga!’ Ndiyeno Mulungu anati: ‘Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekha, muyende ulendo wopita ku phili limene ndidzakuonetsa. Kumeneko ukamuphe mwana wako ndi kumupeleka nsembe.’

Mau amenewa anamucititsa kumvela cisoni kwambili Abulahamu cifukwa anali kumukonda kwambili mwana wake. Ndipo kumbukila kuti Mulungu analonjeza kuti ana a Abulahamu adzakhala mu dziko la Kanani. Koma zimenezi zingacitike bwanji ngati Isaki amwalila? Abulahamu sanamvetsetse zimenezi. Ngakhale zinali conco, iye anamvela Mulungu.

Pamene Abulahamu anafika ku phili, anamanga Isaki ndi kumuika paguwa la nsembe limene anapanga. Ndiyeno anatulutsa mpeni kuti aphe mwana wake. Koma panthawi imeneyo, mngelo wa Mulungu anamuitana kuti: ‘Abulahamu! Abulahamu!’ Iye anayankha kuti: ‘Ine mbuyanga!’

Mulungu anati: ‘Usamuvulaze mwanayo kapena kumucitila ciliconse. Tsopano ndadziŵa kuti uli ndi cikhulupililo mwa ine, pakuti sunakane kupeleka kwa ine mwana wako mmodzi yekha.

Waona kuti Abulahamu anali ndi cikhulupililo colimba mwa Mulungu! Iye anakhulupilila kuti palibe cimene Yehova sangacite, ndi kuti Yehova angaukitse Isaki akamwalila. Komabe sicinali kweni-kweni cifunilo ca Mulungu kuti Abulahamu aphe Isaki. Conco Mulungu anacititsa kuti nkhosa igwilike mu tumitengo tunali pafupi. Ndipo anauza Abulahamu kuti aipeleke nsembe m’malo mwa mwana wake.

Genesis 21:1-7; 22:1-18.