Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 16

Isaki Apeza Mkazi Wabwino

Isaki Apeza Mkazi Wabwino

KODI wamudziŵa mkazi amene ali pacithunzi-thunzi apa? Dzina lake ni Rabeka. Ndipo mwamuna amene akumana naye ni Isaki. Rabeka adzakhala mkazi wake. Kodi zimenezi zinacitika bwanji?

Tate wa Isaki, Abulahamu, anali kufuna kupezela mwana wake mkazi wabwino. Sanafune kuti Isaki akwatile mkazi wocokela ku mtundu wa Akanani, cifukwa anthu amenewo anali kulambila milungu yonama. Conco, Abulahamu anaitana mtumiki wake ndi kumuuza kuti: ‘Ndifuna kuti ubwelele kwa acibanja anga ku Harana, ndipo ukamutengele mkazi mwana wanga Isaki.’

Nthawi imeneyo mtumiki wa Abulahamu anatenga ngamila 10 ndi kuyamba ulendo utali. Pamene anafika pafupi ndi kumene acibanja a Abulahamu anali kukhala, anaima pacitsime. Akazi a mu mudzi anali kubwela pacitsime kudzatapa madzi nthawi ya kumadzulo. Mtumiki wa Abulahamu anapemphela kwa Yehova kuti: ‘Mkazi amene adzanitapila madzi, ndi kutapilanso ngamila zonse, akhale amene mwasankha kukhala mkazi wa Isaki.’

Posapita nthawi, Rabeka anafika kudzatapa madzi. Pamene mtumikiyo anapempha Rabeka madzi akumwa, iye anamupatsa. Ndiyeno anatapanso madzi okwanila ngamila zonse zimene zinali ndi njota. Imeneyi inali nchito yovuta cifukwa ngamila zimamwa madzi ambili.

Pamene Rabeka anatsiliza kucita zimenezi, mtumiki wa Abulahamu anamufunsa dzina la atate ake. Iye anapemphanso ngati ni kotheka kugonako kunyumba kwao. Rabeka anayankha kuti: ‘Ine ndine mwana wa Betuele, komanso malo ogona alipo.’ Mtumiki wa Abulahamu anali kudziŵa kuti Betuele anali mwana wa Nahori, m’bale wa Abulahamu. Conco anagwada pansi ndi kuonga zikomo kwa Yehova cifukwa comutsogolela kwa acibanja a Abulahamu.

Usiku umenewo mtumiki wa Abulahamu anauza Betuele ndi Labani, mlongosi wa Rabeka, cifukwa cake anabwela kwa io. Onse aŵili anavomela kuti Rabeka angayende naye mtumiki ameneyo kuti akakwatiwe kwa Isaki. Kodi Rabeka anakamba ciani pamene anafunsidwa? Iye anati: ‘Inde.’ Anali wofunitsitsa kupita. Conco, tsiku lotsatila anakwela ngamila ndi kuyamba ulendo utali wobwelela ku Kanani.

Anafika ku Kanani kumadzulo kwambili. Rabeka anaona mwamuna akuyenda m’munda. Mwamunayo anali Isaki. Anakondwela kwambili kuona Rabeka, ndipo panali patangopita zaka zitatu kucokela pamene amai ake a Sara anamwalila, ndipo anali akali ndi cisoni. Koma Isaki anamukonda kwambili Rabeka, cakuti anakhalanso wokondwela.

Genesis 24:1-67.