Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 17

Amapasa Amene Anali Osiyana

Amapasa Amene Anali Osiyana

ANYAMATA awiri pano ali osiyana kwambiri, kodi si choncho? Kodi mukudziwa maina ao? Mpalu’yu ndi Esau, ndi mbusa wa nkhosa’yo ndiye Yakobo.

Esau ndi Yabobo anali ana amapasa a Isake ndi Rebeka. Atate’yo, Isake, anakonda kwambiri Esau, chifukwa anali mpalu wabwino ndipo ankadza ndi zakudya za banja’lo. Koma Rebeka anakonda Yakobo kopambana, chifukwa anali mnyamata wofatsa ndi wamtendere.

Gogo Abrahamu anali akali moyo, ndipo tingayerekezere m’mene Yakobo anakondera kumumvetsera akunena za Yehova. Potsiriza Abrahamu anafa ali ndi zaka 175, mapasa’wo ali ndi zaka 15.

Esau ali ndi zaka 40 anakwatira akazi awiri a m’Kanani. Izi zinakwiyitsa kwambiri Isake ndi Rebeka, chifukwa akazi’wa sanalambire Yehova.

Tsiku lina kanthu kena kanachitika kamene kanapsyetsa mtima kwambiri Esau pa mbale wake Yakobo. Nthawi inafika yoti Isake apereke dalitso kwa mwana wake wamkulu. Pakuti Esau anali wamkulu koposa Yakobo, Esau anayembekezera kulandira dalitso’li. Koma Esau anali atagulitsa kuyenera kwa kulandira dalitso’li kwa Yakobo. Ndipo’nso, pa kubadwa kwa ana awiri’wa Mulungu anali atanena kuti Yakobo akalandira dalitso. Ndipo izi ndizo zinachitika. Isake anapereka dalitso’lo kwa mwana wake Yakobo.

Atamva izi Esau anakwiyira Yakobo. Anali wokwiya kwambiri kwakuti anati akapha Yakobo. Atamva izi Rebeka, anada nkhawa kwambiri. Nauza mwamuna wake Isake kuti: ‘Zidzakhala zoopsya’di ngati Yakobo naye’nso akwatira mmodzi wa akazi a Kanani’wa.

Motero anaitana Yakobo mwana wake namuuza kuti: ‘Usakwatire Mkazi wa m’Kanani. Koma upite ku mbumba ya gogo wako Betuele m’Harana. Ukakwatire mmodzi wa ana akazi a mwana wao wamwamuna Labani.’

Yakobo anamvetsera atate wake, pompo ananyamuka kumka kwa abale ake m’Harana.