Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 17

Ana Amapasa Osiyana

Ana Amapasa Osiyana

ANYAMATA aŵili amene uona apa ni osiyana kwambili, kodi si conco? Kodi maina ao wawadziŵa? Wosaka nyama ni Esau, ndipo mnyamata amene alisha nkhosa ni Yakobo.

Esau ndi Yakobo anali amapasa kapena kuti ampundu. Anali ana a Isaki ndi Rabeka. Isaki anali kukonda kwambili Esau, cifukwa anali kudziŵa kusaka nyama ndipo anali kubweletsela banja lao nyama yakudya. Koma Rabeka anali kukonda kwambili Yakobo, cifukwa anali wofatsa ndiponso wamtendele.

Ambuye ao, a Abulahamu, anali akali moyo, ndipo tangoganizila mmene Yakobo anali kukondela kumvetsela kwa Abulahamu pamene anali kufotokoza za Yehova. Abulahamu anamwalila ali ndi zaka 175, pamene ana amapasa amenewo anali ndi zaka 15.

Pamene Esau anakhala ndi zaka 40 anakwatila akazi aŵili acikanani. Zimenezi zinacititsa kuti Isaki ndi Rabeka akhumudwe kwambili, cifukwa akazi amenewa sanali kulambila Yehova.

Ndiyeno tsiku lina, panacitika cinthu cina cimene cinapangitsa Esau kukwiya kwambili kwa Yakobo mng’ono wake. Tsopano inafika nthawi imene Isaki anafunika kudalitsa mwana wake wamkulu. Popeza Esau anali mkulu pa Yakobo, iye anali kuyembekezela kuti ndiye adzadalitsidwa. Koma Esau anali anagulitsa kale ukulu wake kwa Yakobo wakuti alandile dalitso. Ndiponso pamene anyamata amenewa anabadwa, Mulungu anakambilatu kuti Yakobo ndi amene adzalandila dalitso. Ndipo izi ndiye zimene zinacitika. Isaki anadalitsa mwana wake Yakobo.

Panthawi ina, Esau anadziŵa zimenezi ndipo anamukwiyila Yakobo. Iye anakwiya kwambili cakuti ananena kuti adzamupha Yakobo. Pamene Rabeka anamva zimenezi anada nkhawa kwambili. Conco anauza mwamuna wake Isaki kuti: ‘Cidzakhala cinthu coipa kwambili ngati Yakobo nayenso adzakwatila mkazi wacikanani.’

Pamenepo Isaki anaitana Yakobo mwana wake, ndi kumuuza kuti: ‘Usakakwatile mkazi wacikanani. M’malo mwake, pita kunyumba ya ambuye ako a Betuele ku Harana. Kumeneko ukakwatile mmodzi wa ana a Labani.’

Yakobo anamvela zimene atate ake anamuuza, ndipo nthawi imeneyo anayamba ulendo utali wopita kumene acibanja ake anali kukhala, ku Harana.

Genesis 25:5-11, 20-34; 26:34, 35; 27:1-46; 28:1-5; Aheberi 12:16, 17.