Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 18

Yakobo Amka ku Harana

Yakobo Amka ku Harana

KODI mukudziwa amuna awa amene Yakobo akulankhula nawo? Atayenda masiku ambiri, Yakobo anawapeza pafupi ndi chitsime. Iwo anali kuweta nkhosa zao. Yakobo anafunsa kuti: ‘Kwanu n’kuti?’ Iwo anati, ku ‘Harana.’

Yakobo anafunsa kuti, ‘Kodi Labani mumam’dziwa?’

Iwo anayankha kuti, ‘Inde. Uyo, adza apo’yo ndi mwana wake wamkazi Rakele ndi gulu lake la nkhosa.’ Kodi mukuona Rakele akudza chauko’yo?

Pamene Yakobo anaona Rakele ndi nkhosa za malume wake Lebani, anamka nakunkuniza mwala pa chitsime kuti nkhosa zimwe. Ndiyeno Yakobo anapsyompsyona Rakele namuuza kuti iye anali yani. Anali wochititsidwa nthumanzi kwambiri, ndipo anamka kunyumba nauza atate wake Labani.

Labani anali wokondwa kwambiri kuti Yakobo adzakhale naye. Ndipo pamene Yakobo anapempha kuti akwatire Rakele, Labani anakondwa. Komabe, anapempha Yakobo kugwira ntchito m’munda mwake kwa zaka zisanu ndi ziwiri kaamba ka Rakele.

Chifukwa anakonda Rakele kwambiri Yakobo anachita izi. Koma nthawi ya ukwati itakwana, kodi mukudziwa chimene chinachitika?

Labani anapatsa Yakobo mwana wake wamkazi wamkulu Leya m’malo mwa Rakele. Pamene Yakobo anabvomereza kugwirira ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziwiri, anam’patsa’nso Rakele akhale mkazi wake. M’nthawiyo Mulungu analola amuna kukhala ndi akazi oposa mmodzi. Koma tsopano, monga momwe Baibulo likunenera, mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi yekha.