Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 20

Dina Alowa M’bvuto

Dina Alowa M’bvuto

KODI mukuona amene Dina akukacheza nawo? Akumka kukaona atsikana ena okhala m’Kanani. Kodi atate wake akakondwera nazo? Kuti tiyankhe funso’li, tiyeni tikumbukire zimene Abrahamu ndi Isake anaganiza ponena za akazi a m’Kanani.

Kodi Abrahamu anafuna kuti Isake akwatire mtsikana wa M’Kanani? Ai. Kodi Isake ndi Rebeka anafuna kuti mwana wao Yakobo akwatire mtsikana wa m’Kanani? Ai. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

N’chifukwa chakuti Akanani analambira milungu yonyenga. Iwo sanali anthu abwino kukwatiwa nawo kapena kuwakwatira, ndipo sanali anthu abwino kuyanjana nawo. Chotero tingakhale otsimikizira kuti Yakobo sakakondwera kuti mwana wake wamkazi anali kupalana ubwenzi ndi atsikana Achikanani’wa.

Ndithudi, Dina analowa m’bvuto. Kodi mukuona mwamuna Wachikanani uyo amene akuyang’ana Dina? Dzina lake ndi Sekemu. Tsiku lina pamene Dina anadza kudzacheza, Sekemu anam’nyenga nam’kakamiza kugona naye. Izi zinali zolakwa, chifukwatu ndiwo amuna ndi akazi okwatirana okha amene ayenera kugona pamodzi. Choipa chochitidwa ndi Sekemu’chi chinachititsa mabvuto ochuluka kwambiri.

Pamene abale a Dina anamva za chochitika’chi, anapsya mtima kwambiri. Awiri a iwo Simeoni ndi Levi, anakwiya kwambiri kwakuti anatenga malupanga nalowa mu mzinda’wo natulukira amuna’wo modzidzimutsa. Iwo ndi abale ao anapha Sekemu ndi amuna ena onse. Yakobo anapsya mtima chifukwa chakuti ana ake anachita choipa’chi.

Kodi bvuto lonse’li linayamba bwanji? N’chifukwa chakuti Dina anapalana ubwezi ndi anthu osamvera malamulo a Mulungu. Sitidzafuna kupanga mabwenzi otero’wo kodi si choncho?