Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 20

Dina Agwela M’mavuto

Dina Agwela M’mavuto

KODI waona atsikana amene Dina wayenda kukaceza nao? Wayenda kukaona atsikana ena amene akhala ku Kanani. Kodi atate ake a Yakobo adzakondwela akamvela zimenezi? Kuti tiyankhe funso ili, tiyenela kukumbukila mmene Abulahamu ndi Isaki anali kuwaonela akazi acikanani.

Kodi Abulahamu anali kufuna kuti mwana wake Isaki akwatile mtsikana wacikanani? Iyai. Nanga kodi Isaki ndi Rabeka, anafuna kuti mwana wao Yakobo akwatile mkazi wacikanani? Iyai. Kodi udziŵa cifukwa cake?

N’cifukwa cakuti anthu a ku Kanani anali kulambila milungu yonama. Sanali anthu ofunikila kukwatilako kapena kukwatiwako, ndipo sanalinso ofunikila kukhala nao paubwenzi. Conco, tingadziŵe kuti Yakobo sanakondwele kuti mwana wake wamkazi anakhala mnzao wa ana akazi acikanani.

Kukamba zoona, Dina agwela m’mavuto akulu. Kodi wamuona mnyamata wacikanani amene ayang’ana Dina pa cithunzi-thunzi apa? Dzina lake ni Sekemu. Tsiku lina pamene Dina anayenda kukaceza, Sekemu anamugwila ndi kugona naye mwacikakamizo. Kucita zimenezo ni kulakwa, cifukwa amuna ndi akazi okwatilana cabe, ni amene ayenela kugona pamodzi. Cinthu coipa ici cimene Sekemu anacita kwa Dina cinabweletsa mavuto ena ambili.

Pamene azilongosi a Dina anamvela zimene zinacitika, anakalipa kwambili. Aŵili anali Simiyoni ndi Levi. Iwo anakalipa kwambili cakuti anatenga malupanga ndi kuloŵa mumzinda mosaonetsela colinga cao. Iwo pamodzi ndi abale ao, anapha Sekemu ndi amuna ena onse. Yakobo anakhumudwa kwambili ndi cinthu ici cimeneci iwo anacita.

Kodi mavuto onse awa anayamba bwanji? Anayamba pamene Dina anayamba kuseŵela ndi anthu amene sanali kumvela malamulo a Mulungu. Sitifunikila kukhala ndi anzathu amtundu umenewu, kodi si conco?

Genesis 34:1-31.