Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 21

Abale a Yosefe Amuda

Abale a Yosefe Amuda

ONANI m’mene mnyamata’yo aliri wachisoni ndi wopanikizika. Uyu ndi Yosefe. Abale ake angom’gulitsa kumene kwa anthu a pa ulendo omka ku Igupto’wa. Uko Yosefe adzakhala kapolo. Kodi abale ake’wa achitiranji choipa’chi? N’chifukwa cha kuchitira nsanje Yosefe.

Atate wao Yakobo anakonda Yosefe kwambiri. Anam’sonyeza chiyanjo mwa kum’soketsera mwinjiro wokongola. Akulu ake 10 ataona m’mene Yakobo anam’kondera, anayamba kuchita nsanje ndi kuda Yosefe. Koma panali chifukwa china’nso chimene anam’dera.

Yosefe analota maloto awiri. Mu awiri onse’wo abale ake onse anam’gwadira. Pamene Yosefe anauza abale ake maloto’wa, udani wao unaonjezeka kwambiri.

Tsono tsiku lina abale a Yosefe’wo akuweta nkhosa za atate wao, Yakobo akutuma Yosefe kukaona m’mene iwo aliri. Abale ake’wo pomuona akudza, ena akunena kuti: ‘Tiyeni timuphe!’ Koma Rubeni mkulu wa onse, akuti: ‘Ai’ musatero!’ M’malo mwake akum’gwira ndi kum’ponya m’dzenje lopanda madzi. Ndiyeno anakhala pansi kusinkha-sinkha choti am’chitire.

Pa nthawi yomweyi Aismayeli akudza. Yuda akunena ndi abale ake kuti: ‘Tiyeni tim’gulitse kwa Aismayeli.’ Ndipo ndizo’di zimene akuchita. Iwo akugulitsa Yosefe ndi ndalama za siliva 20. Ha, zimene’zo zinali zoipa ndi zopanda chifundo chotani nanga!

Kodi abale’wo akauzanji atate wao? Iwo akupha mbuzi ndi kunyika mwinjiro wokongola wa Yofese’wo m’mwazi wa mbuzi’wo. Ndiyeno akumka ndi malaya’wo kwa Yakobo atate wao nati: ‘Tinawapeza awa pa njira. Aoneni, ngati sali malaya a Yosefe.’

Yakobo akuona kuti ndiwo. ‘Ayenera kukhala atadyedwa ndi chirombo,’ iye akulira. Ndipo izi ndizo zimene’di abale a Yosefe akufuna kuti atate wao aganize. Yakobo ali ndi chisoni kwambiri. Akulira kwa masiku ambiri. Koma Yosefe sanafe. Tiyeni tione zimene zinam’chitikira kumene anatengeredwa’ko.