Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 23

Maloto A Farao

Maloto A Farao

PAPITA zaka ziŵili ndipo Yosefe akali mu ndende. Mpaka pano,wopelekela cikho uja sanamukumbukile. Ndiyeno, usiku wina Farao analota maloto aŵili odabwitsa kwambili, ndipo sanadziŵe tanthauzo lake. Kodi wamuona pacithunzi-thunzi apa ali gone? Tsiku lotsatila, Farao aitana amuna ake anzelu ndipo awauza zimene walota. Koma sanakwanitse kumuuza tanthauzo la zimene walota.

Ndiyeno wopelekela cikho tsopano akumbukila Yosefe. Iye akuti kwa Farao: ‘Pamene ndinali mu ndende, munali munthu wina amene anali kumasulila maloto.’ Pamenepo, Farao atuma anthu kuti akamutenge Yosefe ku ndende.

Farao auza Yosefe maloto ake. Iye akuti: ‘Ndinaona ng’ombe 7 zonenepa ndi zooneka bwino. Ndinaonanso ng’ombe 7 zoonda ndi za maonekedwe onyansa. Ndipo ng’ombe zoonda zinayamba kudya zonenepa zija.

‘Mu loto langa laciŵili ndinaona ngala 7 za tiligu zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi. Ndinaonanso ngala zina 7 zooneka zofoota ndi zoŵauka. Ndiyeno ngala zofootazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwino.’

Yosefe auza Farao kuti: ‘Maloto anu aŵiliwo tanthauzo lake n’limodzi. Ng’ombe 7 zonenepa ndi ngala 7 zooneka bwino ziimila zaka 7. Ng’ombe 7 zoonda ndi ngala 7 zofoota ziimilanso zaka zina 7. Kudzabwela zaka 7 zimene kudzakhala cakudya cambili mu dziko lonse la Iguputo. Ndiyeno padzabwela zaka 7 pamene kudzakhala njala yaikulu.’

Conco, Yosefe auza Farao kuti: ‘Musankhe munthu wozindikila ndi wanzelu, ndipo mumuike kuti aziyang’anila kusonkhanitsidwa kwa cakudya pazaka 7 za zokolola zambili. Pamenepo anthu sadzakhala ndi njala pa zaka 7 zimene kudzakhala njala.’

Farao akondwela ndi zimene Yosefe amuuza. Ndipo asankha Yosefe kuti asonkhanitse cakudya ndi kucisunga. Yosefe akhala ndi udindo waukulu mu dziko la Iguputo, ndipo akhala waciŵili kwa Farao.

Patapita zaka 8, pamene mu dziko mukali njala, Yosefe aona amuna akubwela. Kodi amuna amenewa uwadziŵa? Iwo ni abale ake aja 10. Atate ao, Yakobo anawatuma ku Iguputo cifukwa cakudya cinatha kwao ku Kanani. Yosefe awakumbukila abale ake, koma io sanamudziŵe. Kodi udziŵa cifukwa cake? Ni cifukwa cakuti Yosefe wakula, ndipo wavala zovala zosiyana ndi zao.

Yosefe akumbukila kuti pamene anali mwana analota abale ake akubwela kwa iye ndi kumugwadila. Kodi waikumbukila nkhani imeneyi? Conco Yosefe aona kuti ndi Mulungu amene anamutumiza ku Iguputo. Ndipo aona kuti anamutumiza pa cifukwa cabwino. Kodi uganiza Yosefe anacita ciani? Tiye tione.

Genesis 41:1-57; 42:1-8; 50:20.