Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 24

Yosefe Ayesa Abale Ake

Yosefe Ayesa Abale Ake

YOSEFE akufuna kudziwa ngati abale ake 10 akali oipa ndi opanda chifundo. Chotero akuti: ‘Inu ndinu azondi. Mwadza kudzaona pofoka pa dziko lathu.’

Iwo akuti, ‘Ai.’ ‘Ndife anthu osanyenga. Tonse ndife abale. Tinalipo 12. Koma mmodzi kulibe’nso, ndipo wamng’ono ali ndi atate kwathu.’

Yosefe akuchita ngati sakuwakhulupirira. Akuika m’ndende mbale wochedwa Simeoni, nalola enawo kutenga chakudya n’kupita kwao. Koma akuwauza kuti: ‘Pobwera’nso mudze ndi mng’ono wanu.’

Pofika kwao m’Kanani, abale’wo akusimbira atate wao Yakobo chochitika chiri chonse. Yakobo ali wachisoni kwambiri. ‘Yosefe kulibe’nso,’ akulira, ‘ndipo Simeoni kulibe’nso. Sindidzakulolani kutenga mwananga wamng’ono’yu Benjamini.’ Koma pamene chakudya chao chikutha, Yakobo akuwalola kutenga Benjamini kumka ku Igupto kuti akapeze chakudya china.

Tsono Yosefe akuona abale ake akudza. Ali wokondwa kuona mng’ono wake Benjamini. Zedi, palibe ali yense wa iwo akudziwa kuti munthu wofunika’yu ndi Yosefe. Tsopano iye akuchita kanthu kena kuyesa abale ake 10.

Akuchititsa atumiki ake kudzaza matumba ao zakudya. Mosadziwa iwo, akuika’nso chikho chake cha siliva m’thumba la Benjamini. Iwo onse atachoka ndi kuyenda kamtunda pang’ono, Yosefe akutuma mtumiki wake kuwatsatira. Atawapeza, mtumiki’yo akuti: ‘Mwaberanji chikho cha siliva cha mbuyathu?’

Iwo onse anati, ‘Sitinabe chikho ife.’ Mukachipeza mwa mmodzi wa ife, aphedwe munthu’yo.’

Tsono mtumiki’yo akufuna-funa m’matumba onse, ndipo akupeza chikho’cho m’la Benjamini, monga mukuonera pano. Mtumiki’yo akuti: ‘Nonsenu mungapite, koma Benjamini adzabwerera nafe.’ Kodi abale 10’wo adzachitanji tsono?

Onse akubwerera ndi Benjamini ku nyumba ya Yosefe. Iye akuuza abale ake’wo kuti: ‘Nonse mungapite kwanu, koma Benjamini adzakhala kapolo wanga.’

Yuda tsopano akunena, kuti: ‘Ndikabwerera kwathu popanda mnyamata’yo atate adzafa chifukwa amam’konda kwambiri. Chotero chonde, tengani ine ndikhale kapolo wanu, koma lolani uyu apite.’

Yosefe akuona kuti abale ake asintha. Iwo sali ouma mtima ndi opanda chifundo. Tiyeni tione chimene Yosefe akuchita tsono.