Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 26

Yobu Akhalabe Wokhulupilika Kwa Mulungu

Yobu Akhalabe Wokhulupilika Kwa Mulungu

KODI umvela cifundo kuona munthu wodwala uyu? Dzina lake ni Yobu, ndipo ali ndi mkazi wake. Kodi udziŵa zimene mkaziyu auza mwamuna wake Yobu? Iye akuti: ‘Tukanani Mulungu kuti mufe!’ Tiye tione cifukwa cake akamba zinthu zimenezi, ndiponso tione cifukwa cake Yobu avutika kwambili.

Yobu anali munthu wokhulupilika ndi womvela Yehova. Iye anali kukhala ku dziko la Uzi, pafupi ndi Kanani. Yehova anali kumukonda kwambili Yobu, koma panali winawake amene anali kumuzonda. Kodi ungamudziŵe ameneyu?

Anali Satana Mdyelekezi. Kumbukila kuti Satana ni mngelo woipa amene amazonda Yehova. Iye anacititsa Adamu ndi Hava kuti apandukile Yehova. Satana anali kuganiza kuti angapangitse anthu onse kupandukila Yehova. Kodi anakwanitsa kucita zimenezi? Iyai. Yesa kukumbukila amuna ndi akazi ambili amene taphunzila. Kodi ungachuleko angati?

Pamene Yakobo ndi Yosefe anamwalila ku Iguputo, Yobu ndiye munthu amene anakhala wokhulupilika kwambili kwa Yehova padziko lonse lapansi. Yehova anali kufuna kuti Satana adziŵe kuti sangakwanitse kupangitsa anthu onse kukhala oipa. Conco anati kwa Satana: ‘Wamuona Yobu, iye ndi wokhulupilika kwa ine.’

Koma Satana anayankha kuti: ‘Iye ni wokhulupilika cifukwa mwamudalitsa, ndipo ali ndi zinthu zabwino zambili. Koma mukamulanda zimenezi, adzakutukanani.’

Conco Yehova anati: ‘Cabwino, cita zoipa zonse zimene ufuna kucita kwa Yobu. Umulande zinthu zabwino zonse zimene ali nazo, ndipo tidzaona ngati adzanitukana. Koma cabe usamuphe.’

Coyamba, Satana anacititsa anthu kuba ng’ombe ndi ngamila za Yobu, ndipo anapha nkhosa zake zonse. Ndiyeno anaphanso ana ake 10, amuna ndi akazi ndi cimphepo. Ndiponso anadwalitsa Yobu matenda oopsa, cakuti Yobu anavutika kwambili. Cifukwa ca zimenezi mkazi wake anamuuza kuti: ‘Tukanani Mulungu kuti mufe.’ Koma Yobu sanacite zimenezo. Ndiponso, anzake atatu abodza anabwela ndi kumuuza kuti panali zinthu zoipa zimene Yobu anali kucita kumbali. Koma Yobu anapitiliza kukhala wokhulupilika.

Zimenezi zinamukondweletsa kwambili Yehova, cakuti pambuyo pake anadalitsa Yobu, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi. Yehova anacilitsa matenda ake. Yobu anakhalanso ndi ana ena 10 okongola, anakhalanso ndi ng’ombe, nkhosa ndi ngamila kuwilikiza kaŵili pa zimene anali nazo poyamba.

Kodi iwe udzakhala wokhulupilika nthawi zonse kwa Yehova monga Yobu? Ngati udzatelo, Mulungu adzakudalitsa nawenso. Udzakhoza kukhala ndi moyo wamuyaya pamene dziko lonse lapansi lidzakhala lokongola monga munda wa Edeni.

Yobu 1:1-22; 2:1-13; 42:10-17.