Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 27

Mfumu Yoipa Ilamula Igupto

Mfumu Yoipa Ilamula Igupto

AMUNA’WA pano akuumiriza anthu kugwira ntchito. Mukuona uyo amene akumenya n’chikoti mmodzi wa antchito’wo! Antchito’wo ali a banja la Yakobo, ochedwa Aisrayeli. Oumiriza ntchito’wo ndiwo Aigupto. Aisrayeli akhala akapolo a Aigupto. Kodi zinachitika motani?

Kwa zaka zambiri banja lalikulu la Yakobo linali mu mtendere mu Igupto. Yosefe, amene anali wachiwiri kwa mfumu Farao uja, anawasamalira. Komano Yosefe anafa. Ndipo Farao watsopano amene sanakonde Aisrayeli, anakhala mfumu mu Igupto.

Chotero Farao woipa’yu anapanga Aisrayeli kukhala akapolo. Naika amuna owayang’anira amene anali oipa ndi ankhanza. Iwo anakakamiza Aisrayeli kugwira ntchito zolimba kumangira Farao mizinda. Koma Aisrayeli anapitirizabe kuonjezeka. Katapita kanthawi Aigupto anaopa kuti Aisrayeli akakhala ochuluka kwambiri ndi amphamvu kwambiri.

Kodi mukudziwa chimene Farao anachita? Anauza akazi othandiza amai Achiisrayeli pobala ana kuti: ‘Muzipha mwana wamwamuna ali yense wobadwa.’ Koma awa anali akazi abwino, ndipo sanaphe ana’wo.

Chotero Farao analamula anthu ake onse kuti: ‘Iphani makanda achimuna a Israyeli. Siyani ana akazi okha.’ Kodi izi sizinali zoopsya kuzilamula? Tiyeni tione m’mene mwana wamwamuna wina anapulumutsidwira.