Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 27

Mfumu Yoipa Ilamulila Ku Iguputo

Mfumu Yoipa Ilamulila Ku Iguputo

AMUNA amene uona pacithunzi-thunzi apa akakamiza anthu kuseŵenza. Wamuona mwamuna uyu amene akwapula anthu amene aseŵenza? Anthu amenewa ni a banja la Yakobo, ndipo amachedwa Aisiraeli. Koma amuna amene awakakamiza kuseŵenza ni Aiguputo. Aisiraeli anakhala akapolo ku Iguputo. Kodi anakhala bwanji akapolo?

Kwa zaka zambili, banja lalikulu la Yakobo linali kukhala mwa mtendele ku Iguputo. Yosefe anali ndi udindo waukulu kwambili mu dziko la Iguputo. Popeza anali waciŵili kwa Farao, ndi amene anali kuwasamalila. Koma Yosefe anamwalila. Ndipo Farao watsopano, amene sanali kukonda Aisiraeli, anakhala mfumu ku Iguputo.

Conco, Farao woipa ameneyu anapanga Aisiraeli kukhala akapolo. Ndipo anaika anthu ouma mtima ndi ankhanza kuti aziwayang’anila. Anthu amenewa anali kukakamiza Aisiraeli kuseŵenza kwambili kumangila Farao mizinda. Ngakhale ni conco, Aisiraeli anapitilizabe kuculuka. Patapita nthawi, Aiguputo anacita mantha kuti Aisiraeli adzaculuka kwambili, cakuti angadzakhale ndi mphamvu kuwapambana.

Kodi udziŵa cimene Farao anacita? Anauza anamwino, kapena kuti azimai aciisilaeli othandiza akazi pobeleka, kuti: ‘Mwana mwamuna aliyense akabadwa muzimupha.’ Koma anamwino amenewa anali a mitima yabwino, ndipo sanali kupha tuŵana tobadwa.

Conco Farao anapeleka lamulo kwa anthu onse lakuti: ‘Muzitenga ana amuna aciisiraeli ndi kuwapha, Koma ana akazi osawapha.’ Kukamba zoona, lamulo limeneli linali loipa kwambili! Tiye tione mmene kamwana kena kanapulumukila.

Ekisodo 1:6-22.