Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 28

Mmene Kamwana, Ka Mose, Kanapulumukila

Mmene Kamwana, Ka Mose, Kanapulumukila

KODI wakaona kamwana kamene kalila, ndipo kagwililila cala, kapena kuti cikumo ca mai uyu? Kamwana kameneka ni ka Mose. Kodi wamudziŵa mtsikana wokongola uyu? Ni mwana wa mfumu Farao.

Mai wake anamubisa Mose kufikila pamene anakwanitsa miyezi itatu, cifukwa sanafune kuti Aiguputo amuphe. Koma cifukwa anali kudziŵa kuti Aiguputo angamupeze, anamubisa kuti amupulumutse.

Mai wa Mose anatenga basiketi ndi kuikonza bwino-bwino kuti madzi asaloŵemo. Ndiyeno anaika ka Mose mu basiketi ndi kuibisa pamaudzu atali m’mbali mwa mtsinje wa Nailo. Miriamu, mlongosi wa Mose, anauzidwa kuti aime capafupi kuti aziona zimene zingacitike kwa kamwanako.

Patapita kanthawi, mwana mkazi wa Farao anafika kumtsinje wa Nailo kuti asambe. Mwadzidzidzi, anaona basiketi pamaudzu atali. Anaitana mmodzi wa atsikana ake omutumikila, ndi kumuuza kuti: ‘Nibweletsele basiketi iyo.’ Pamene mwana wa Farao anatsegula basiketi, anapezamo kamwana kokongola kwambili. Kamwanako kanali kulila, ndipo mwana wa Farao anakamvelela cifundo. Sanafune kuti kamwana aka kaphedwe.

Ndiyeno Miriamu anafika pamene io anali. Ni uyu ali pacithunzi-thunzi apa. Miriamu anafunsa mwana wa Farao kuti: ‘Kodi mufuna kuti nikuitanileni mkazi waciisiraeli kuti akuleleleni mwana uyu?’

Mwana wa Farao anati: ‘Inde cita zimenezo.’

Mwamsanga Miriamu anathamanga kukauza amai ake. Pamene amai a Mose anafika kwa mwana wa Farao, iye anawauza kuti: ‘Tenga mwana uyu ukanilelele, ndipo ine nizikulipila.’

Conco, mai wa Mose anali kusamalila mwana wake-wake. Pamene Mose anakula, mai wake anamubweza kwa mwana wa Farao. Ndipo iye anamutenga kukhala mwana wake. Umu ndi mmene zinacitikila kuti Mose akulile mu nyumba ya Farao.

Ekisodo 2:1-10.