Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 30

Chitsamba Choyaka Moto

Chitsamba Choyaka Moto

MOSE anali atafika ku phiri la Horebi kudzapezera nkhosa zake nsipu. Pano iye anaona chitsamba chikuyaka moto, koma chosanyeka!

‘Izi n’zodabwitsa,’ anaganiza choncho Mose. ‘Ndidzasendera pafupi ndikaonetsetse.’ Atatero, mau anachokera m’chitsamba’cho, akuti: ‘Usayandikire pano. Bvula nsapato zako, chifukwa waima pa malo oyera.’ Anali Mulungu amene analankhula mwa njira ya mngelo, chotero Mose anaphimba nkhope yake.

Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ndaona kubvutika kwa anthu anga m’Igupto. Chotero ndidzawalanditsa, ndipo iwe ndi amene ndidzakutuma kukawatulutsa m’Igupto.’ Yehova akalowetsa anthu ake m’Kanani wokongola’yo.

Mose anati: ‘Ine ndine yani. Kodi ndingachite izi motani? Koma tiyeni titi ndapita. Aisrayeli nadzati kwa ine, “Wakutuma ndani?” pamenepo ndidzanenanji?’

‘Izi ndizo zimene ukanene,’ anayankha motero Yehova. ‘“YEHOVA Mulungu wa Abrahamu, wa Isake ndi wa Yakobo wandituma kwa inu.”’ Yehova anati’nso: ‘Iri ndiro dzina langa kosatha.’

‘Koma tiyeni titi sakundikhulupirira nditanena kuti mwandituma,’ anatero Mose.

Mulungu anafunsa kuti, ‘M’dzanja lako muli chiani?’

Mose anayankha kuti: ‘Ndodo.’

Mulungu anati, ‘Iponye pansi.’ Ataiponya inasanduka njoka. Kenako anam’sonyeza chozizwitsa china. Iye anati: ‘Ika dzanja lako mu mkanjo wako.’ Mose anachita, ndipo potulutsa dzanja lake, linali loyera ngati chipale! Dzanja linaoneka ngati linali ndi khate. Kenako Yehova anam’patsa mphamvu ya kuchita chozizwitsa chachitatu. Nati: ‘Aisrayeli akakaona zozizwitsa’zi adzakhulupirira kuti ndakutuma.’

Ndiyeno Mose anamka kwa Yetero nati: ‘Chonde ndiloleni ndimke kwa achibale anga m’Igupto ndikaone m’mene aliri.’ Yetero anayankha nati pita bwino, ndipo Mose ananyamuka kubwerera ku Igupto.