Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 31

Mose Ndi Aroni Aonana Ndi Farao

Mose Ndi Aroni Aonana Ndi Farao

PAMENE Mose anabwelela ku Iguputo, anauza mkulu wake Aroni zozizwitsa zonse zimene zinacitika. Ndipo pamene Mose ndi Aroni anaonetsa Aisiraeli zozizwitsa zimenezo, anthu onse anakhulupilila kuti Yehova anali nao.

Ndiyeno Mose ndi Aroni anayenda kukaonana ndi Farao. Iwo anamuuza kuti: ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wakamba kuti, “Lolani anthu anga ayende ulendo wa masiku atatu, kuti akandilambile ine mu cipululu.”’ Koma Farao anayankha kuti: ‘Sindikhulupilila Yehova. Ndipo sindidzalola kuti Aisiraeli ayende.’

Farao anakalipa kwambili pamene anthu anapempha nthawi yakuti akalambile Yehova. Conco Farao anawakakamiza kuti aziseŵenza kwambili kuposa kale. Aisiraeli anapatsa mlandu Mose pa nkhanza zimene Farao anali kuwacitila, koma Mose anawamvelela cifundo. Tsopano Yehova anauza Mose kuti asade nkhawa. Anati kwa iye: ‘Ndidzacititsa Farao kulola anthu anga kuti apite.’

Mose ndi Aroni anayenda kukaonananso ndi Farao. Paulendo uwu, io anacita cozizwitsa. Aroni anaponya ndodo yake pansi, ndipo inasanduka njoka yaikulu. Koma amuna anzelu a Farao naonso anaponya pansi ndodo zao, ndipo nazo zinasanduka njoka. Koma ona! Njoka ya Aroni ikudya njoka za amuna anzelu a Farao. Ngakhale n’conco, Farao sanawalole Aisiraeli kuti apite.

Ndiyeno nthawi inakwana yakuti Yehova akhaulitse Farao. Kodi udziŵa zimene anacita? Anabweletsa milili 10, kapena kuti mavuto akulu mu Aiguputo.

Pamene milili yambili inacitika, Farao anatuma anthu ake kuti akaitane Mose, ndipo anati: ‘Leketsani milili, ndipo ndidzalola Aisiraeli kuti ayende.’ Koma milili ikaleka, Farao anali kusintha maganizo ake. Iye sanali kuwalola Aisiraeli kuti apite. Koma potsilizila pake, pamene mlili wa namba 10 unacitika, Farao anawalola Aisiraeli kupita.

Kodi uidziŵa milili yonse 10 imene inacitika? Tsegula peji yotsatila kuti tiphunzile za milili imeneyi.

Ekisodo 4:27-31; 5:1-23; 6:1-13, 26-30; 7:1-13.