Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 32

Miriri 10

Miriri 10

TAYANG’ANANI pa zithunzi’zo. Chiri chonse chikusonyeza mliri wodzetsedwa ndi Yehova pa Igupto. M’choyamba’cho mungathe kuona Aroni akumenya Mtsinje wa Nile ndi ndodo. Atatero, madzi ake anasanduka mwazi. Nsomba zinafa, mtsinje’wo nuyamba kununkha.

Kenako, Yehova anachititsa achule kutuluka mu Nile. Iwo anali pali ponse—m’mauvuni, zophikira, m’makama a anthu—pali ponse. Achule’wo atafa Aigupto anawasokhanitsa m’miyulu yalikulu, ndipo dziko’lo linanunkhitsidwa nawo.

Ndiyeno Aroni anamenya pansi ndi ndodo yake, ndipo pfumbi linasanduka nsabwe, Nsabwe’zo zinali mliri wachitatu pa dziko la Igupto.

Miriri yotsatirapo inabvulaza Aigupto okha, osati Aisrayeli. Wachinai unali mliri wa mizaza imene inalowa m’nyumba zonse za Aigupyo. Mliri wachisanu unali pa zinyama. Ng’ombe, nkhosa ndi mbuzi zambiri za Aigupto zinafa.

Kenako, Mose ndi Aroni anatenga phulusa naliwaza mu mpweya. Iwo anachititsa zironda zowawa pa anthu ndi zinyama. Uwu unali mliri wachisanu ndi chimodzi.

Pambuyo pake Mose anatambasulira dzanja lake kumwamba, ndipo Yehova anatumiza mphezi ndi matalala. Inali mvula ya matalala yoipitsitsa imene Igupto anali asanakhale nayo kale.

Mliri wachisanu ndi chitatu unali dzombe lochuluka kwambiri. Ndi kale lonse nthawi’yo isanakwane kapena kufikira lero sipanakhale dzombe lochuluka chotero. Iro linadya chiri chonse chosiyidwa chosaonongedwa ndi matalala.

Mliri wachisanu ndi chinai unali mdima. Kwa masiku atatu mdima waukulu unakuta dziko’lo, koma Aisrayeli anali ndi kuunika kumene anali.

Potsiriza, Mulungu anauza anthu ake kuwaza mwazi wa msoti wa mbuzi kapena mwana wankhosa pa mphuthu za nyumba zao. Ndiyeno mngelo wa Mulungu anayenda mu Igupto. Poona mwazi’wo, mngelo’yo sanaphe ali yense m’nyumba’yo. Koma m’zonse zopanda mwazi pa mphuthu, mngelo’yo anapha ana oyamba kubadwa a anthu ndi zinyama zomwe. Uwu unali mliri wa 10.

Utapita mliri’wu Farao anauza Aisrayeli kuchoka. Anthu a Mulungu anali okonzeka kupita, ndipo usiku womwewo anayamba ulendo wao wotuluka m’Igupto.