Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 33

Kuoloka Nyanja Yofiila

Kuoloka Nyanja Yofiila

HA, ONA zimene zicitika apa! Uyu ni Mose amene watambasulila ndodo yake kusontha pa Nyanja Yofiila. Anthu amene anapulumuka nao ku mbali ina iyi ni Aisiraeli. Koma Farao ndi magulu ake a nkhondo anambila mu Nyanja. Tiye tione mmene zimenezi zinacitikila.

Monga mmene tinaphunzilila, Farao anauza Aisiraeli kucoka ku Iguputo pambuyo pakuti Mulungu wabweletsa mlili wa namba 10 pa Aiguputo. Pa anthu amene anacoka ku Iguputo panali amuna 600,000, aciisiraeli, kuonjezela pamenepa panalinso akazi ndi ana. Aiguputo ena ambili amene anayamba kukhulupilila Yehova naonso anacoka pamodzi ndi Aisiraeli. Anthu onse amene anacoka anatenga nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zao.

Aisiraeli akalibe kucoka, anapempha Aiguputo zovala ndi zinthu zopangidwa ndi golide ndi siliva. Aiguputo anacita mantha kwambili cifukwa ca mlili wotsiliza umene unawagwela. Conco, anapatsa Aisiraeli zonse zimene anapempha.

Patapita masiku ocepa, Aisiraeli anafika ku Nyanja Yofiila. Pamene anafika kumeneko, anapumula. Pa nthawi imeneyi, Farao ndi anthu ake anamva kuipa kuti analekelela Aisiraeli kucoka. Iwo anati: ‘Talola akapolo athu kucoka!’

Conco Farao anasinthanso maganizo ake. Mwamsanga anatenga galeta yake ya nkhondo ndi kukonzekeletsa gulu lake la nkhondo. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa Aisiraeli ndi magaleta 600 apadela, kuphatikizapo magaleta ena onse a mu Iguputo.

Pamene Aisiraeli anaona kuti Farao ndi gulu lake la nkhondo aŵathamangitsa, anacita mantha kwambili. Panalibe kothaŵila cifukwa kutsogolo kwao kunali Nyanja Yofiila, ndipo kumbuyo kunali Aiguputo. Koma Yehova anaika mtambo wochinjiliza pakati pa anthu ake ndi Aiguputo. Conco Aiguputo sanawacite kanthu Aisiraeli cifukwa sanali kuwaona.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kutambasulila ndodo yake kusontha pa Nyanja Yofiila. Pamene anacita zimenezi, Yehova anacititsa cimphepo camphamvu ca kum’mawa kuomba. Madzi a mu nyanja anagaŵikana, ndipo madziwo anaima ngati zipupa uku ndi uku.

Ndiyeno Aisiraeli anayamba kuoloka nyanja panthaka youma. Kuti anthu onse mamiliyoni, pamodzi ndi ziŵeto zao zonse aoloke bwino-bwino kukafika ku tsidya lina, panapita nthawi yaitali. Potsilizila pake, Aiguputo anayamba kuwaonanso Aisiraeli. Pamene Aiguputo anaona kuti Aisiraeli akuoloka, nao anathamangila pa nyanja kuti awapeze, cifukwa anaona kuti akapolo ao akuthaŵa.

Pamene anacita zimenezi, Mulungu anacititsa mawilo a magaleta ao kuguluka. Aiguputo anacita mantha kwambili, ndipo anayamba kulila kuti: ‘Yehova amenyela nkhondo Aisiraeli. Tiyeni tithaŵe!’ Koma anali atacedwa kale.

Apa m’pamene Yehova anauza Mose kutambasulila ndodo yake kusontha pa Nyanja Yofiila, monga mmene waonela pacithunzi-thunzi. Ndipo pamene Mose anacita zimenezi, madzi anayamba kukumana, ndipo Aiguputo onse ndi magaleta ao anambila. Gulu lonse la nkhondo linatsatila Aisiraeli pa nyanja, ndipo panalibe mmodzi wa Aiguputo amene anapulumuka.

Anthu a Mulungu onse anakondwela kwambili cifukwa cakuti anapulumuka. Amuna anaimba nyimbo yoyamikila Yehova, kuti: ‘Yehova wapeza cipambano caulemelelo. Wambiza mu nyanja mahosi ndi okwelapo ake.’ Mlongosi wa Mose, Miriamu, anatenga masece ake, akazi onse anamutsatila ndi masece ao. Pamene anavina mokondwela, io anaimba nyimbo yofanana ndi imene amuna anaimba kuti: ‘Yehova wapambana. Waponya mahosi ndi okwelapo ake mu nyanja.’

Ekisodo caputa 12 mpaka 15.