Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 34

Mtundu Watsopano wa Chakudya

Mtundu Watsopano wa Chakudya

KODI munganene zimene anthu’wo akutola pansi’po? Ziri ngati chipale. N’zoyera, n’zopyapyala ndi zong’azimira. Koma si chipale’ n’chakudya.

Pangopita mwezi umodzi wokha chichokere Aisrayeli mu Igupto. Iwo ali m’chipululu. Mumamera zakudya zochepa, chotero anthu’wo akudandaula, kuti: ‘Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera m’Igupto. Kuja’ko tinali ndi zakudya zonse zimene tinazifuna.’

Chotero Yehova akuti: ‘Ndidzachititsa chakudya kugwa kuchokera kumwamba.’ Ndipo ndizo’di zimene Yehova akuchita. M’mawa mwake Aisrayeli poona zinthu zoyera’zi zimene zagwa, akufunsana kuti: ‘Ichi n’chiani?’

Mose akuti: ‘Ichi n’chakudya chimene Yehova wakupatsani kuti mudye.’ Anthu’wo akuchicha MANA. Akukoma mofanana ndi mikate yaphanthi-panthi yosanganizidwa ndi uchi.

‘Muzitola wokwanira kudya munthu ali yense,’ anatero Mose kwa anthu’wo. Chotero m’mawa uli wonse izi ndizo zimene iwo akuchita. Dzuwa likatentha, mana wotsala panthaka akusungunuka.

Mose akuti’nso: ‘Palibe ali yense ayenera kusunga mkute wa mana mpaka mawa.’ Koma anthu ena sakumvera. Kodi mukudziwa chimene chikuchitika? Mana wotsala’yo ali mphutsi nyakatu-nyakatu, ndipo akuyamba kununkha!

Komabe, pali tsiku limodzi la sabata liri lonse, limene Yehova akuuza anthu kutola mana wowirikiza. Iri ndiro tsiku lachisanu ndi chimodzi. Ndipo Yehova akulamula kum’sungira m’mawa mwake, chifukwa sadzam’chititsa kugwa pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Pamene akusunga kudzafika pa tsiku lachisanu ndi chiwiri’lo, sakukhala ndi mphutsi ndi kununkha! Ichi n’chozizwitsa china!

Zaka zonse zimene Aisrayeli ali m’chipululu Yehova akuwadyetsa mana.