Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 34

Cakudya Catsopano

Cakudya Catsopano

KODI udziŵa zimene anthu awa ayola pansi? Zioneka monga mame olimba. N’zoyela, zooneka monga unga. Koma si mame iyai, ni cakudya.

Papita pafupi-fupi mwezi umodzi kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo. Apa ali mu cipululu. Mu cipululu simumamela-mela cakudya, conco anthu adandaula kuti: ‘Cikanakhala bwino ngati Yehova anatipha ku Iguputo. Kuja tinali ndi cakudya ciliconse cimene tinali kufuna.’

Conco Yehova akamba kuti: ‘Ndidzagwetsa cakudya kucokela kumwamba.’ Ndipo izi n’zimene Yehova wacita. Tsiku lotsatila kum’mawa, pamene Aisiraeli aona zinthu zoyela zimene zagwa, afunsana kuti: ‘Nanga ici n’ciani?’

Mose awauza kuti: ‘Ici ni cakudya cimene Yehova wakupatsani.’ Iwo apatsa cakudya cimeneco dzina lakuti MANA. Cakudya ici cimveka monga makeke amene athilako uci.

Mose auza anthu kuti: ‘Muziyola cakudya cimene munthu aliyense angakwanitse kudya.’ Conco tsiku lililonse kum’mawa, io anayola cakudya cimeneco. Koma dzuŵa likatentha, mana otsala pansi anali kusungunuka.

Ndiponso Mose awauza kuti: ‘Munthu aliyense asasiyeko mana akuti akadye tsiku lotsatila.’ Koma anthu ena samvela. Kodi udziŵa zimene zicitika? Tsiku lotsatila m’mawa, apeza kuti mana amene anasiyako ali ndi vikusi cakuti ayamba kununkha.

Koma pali tsiku limodzi pawiki limene Yehova auza anthu kuti aziyola mana kuculukitsa kaŵili. Tsiku limenelo ni la 6. Ndipo Yehova awauza kuti azisungako mana tsiku lotsatila, cifukwa patsiku la 7 Mulungu sazigwetsa mana alionse kucokela kumwamba. Iwo akasunga mana kufika tsiku la 7, si akhala ndi vikusi ndipo sanunkha. Ici n’cozizwitsa cina.

Pazaka zonse zimene Aisiraeli akhala mu cipululu, Yehova awadyetsa mana.

Ekisodo 16:1-36; Numeri 11:7-9; Yoswa 5:10-12.