Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 35

Yehova Apereka Malamulo Ake

Yehova Apereka Malamulo Ake

PAFUPI-FUPI miyezi iwiri atatuluka mu Igupto, Aisrayeli akufika pa Phiri la Sinai, limene likuchedwa’nso Horebi. Ndi pa malo omwewa pamene Yehova analankhulapo ndi Mose m’chitsamba choyaka moto. Anthu anamanga mahema pano nakhalapo kwa kanthawi.

Anthu akuyembekezera pansipo, Mose akukwera m’phirimo. Pamwambapo, Yehova akuuza Mose kuti Iye akufuna kuti Aisrayeli amvere Iye ndi kukhala anthu Ake apadera. Pamene Mose akutsika, akuuza Aisrayeli zimene Yehova wanena. Anthu’wo akuti adzamvera Yehova, chifukwa akufuna kukhala anthu ake.

Yehova tsopano akuchita chinthu chodabwitsa. Akuchititsa pamwamba pa phiri’lo kuchita utsi, ndi mphezi. Iye akulankhula’nso ndi anthu’wo kuti: ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Igupto.’ Nawalamula kuti: ‘Musamalambira milungu ina koma ine ndekha.’

Iye akupatsa Aisrayeli malamulo ena asanu ndi anai. Anthu’wo akuopa kwambiri. Iwo akuuza Mose kuti: ‘Inu mulankhule nafe, chifukwa tiopa kuti ngati Mulungu alankhula nafe tingafe.’

Kenako Yehova akuuza Mose kuti: ‘Kwera ku phiri kuno. Ndidzakupatsa miyala iwiri yaphanthi-panthi imene ndalembapo malamulo amene ndikufuna kuti anthu awasunge.’ Chotero Mose akukwera’nso ku phiri. Akukhalako kwa mausana ndi mausiku 40.

Mulungu ali ndi malamulo ochuluka kwambiri kaamba ka anthu ake. Mose akulemba malamulo’wa. Mulungu akum’patsa’nso miyala iwiri’yo. Mulungu mwini walembapo malamulo 10 amene iye ananena ndi anthu onse. Iwo akuchedwa Malamulo Khumi.

Iwo ali malamulo ofunika. Chimodzi-modzi’nso malamulo ena ambiri’wo amene Mulungu anapatsa Israyeli. Limodzi la malamulo’wa ndiro: ‘Udzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, maganizo ako onse, moyo wako wonse ndi nyonga yako yonse.’ Lina ndiro: ‘Udzikonda mnansi wako monga momwe umadzikondera.’ Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anati awa ndiwo malamulo awiri akulu kopambana amene Yehova anapatsa anthu ake Israyeli. Kenako tidzaphunzira zinthu zambiri ponena za Mwana wa Mulungu ndi ziphunzitso zake.