Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 38

Azondi 12

Azondi 12

TAONANI zipatso zimene amuna’wa anyamula. Taonani kukula kwa tsango la mphesa’zo. Litofunikira anthu awiri kulinyamula mopika. Ndipo taonani nkhuyu’zo ndi makangaza. Kodi chipatso chokongola’chi chinachokera kuti? Ku dziko la Kanani. Pajatu, Kanani ndiko kumene Abrahamu, Isake ndi Yakobo anakhala pa nthawi ina. Koma chifukwa cha njala kumene’ko, Yakobo ndi banja lake, anasamukira ku Igupto. Tsopano, zaka 216 pambuyo pake, Mose akutsogolera Aisrayeli kubwerera ku Kanani. Iwo afika pa malo m’chipululu’cho ochedwa Kadesi.

Anthu oipa anakhala m’kanani. Chotero Mose akutumiza azondi 12, nawauza kuti: ‘Kaoneni kuchuluka kwa anthu kumene’ko, ndi m’mene aliri amphamvu. Kaoneni ngati dziko’lo liri la dzinthu. Ndipo katengeni zina za zipatso zake.’

Pamene azondi’wo akubwerera ku Kadesi, akuuza Mose kuti: ‘Ndi dziko labwino’di.’ Ndipo kuti asonyeze, iwo akusonyeza Mose zina za zipatso’zo. Koma 10 mwa azondi’wo akuti: ‘Anthu okhalamo ndi akulu-akulu ndi amphamvu. Tidzaphedwa ngati tiyesa kulanda dziko’lo.’

Aisrayeli akuopa pakumva izi. ‘Kukanakhala bwino kufera mu Igupto kapena ngakhale m’chipululu muno,’ iwo akutero. ‘Tidzaphedwa m’nkhondo, ndipo akazi ndi ana athu adzagwidwa. Tiyeni tisankhe m’tsogoleri watsopano m’malo mwa Mose, ndi kubwerera ku Igupto!’

Koma awiri mwa azondi’wo akudalira mwa Yehova, ndipo akuyesa kutontholetsa anthu’wo. Maina ao ndiwo Yoswa ndi Kalebi. Iwo akuti: ‘Musaope. Yehova ali nafe. Kudzakhala kosabvuta kulanda dziko’lo.’ Koma anthu’wo sakumvetsera. Akufuna kupha Yoswa ndi Kalebi.

Izi zikukwiyitsa Yehova, ndipo akuuza Mose kuti: ‘Palibe ali yense wa anthu’wa woyambira pa zaka 20 ndi kuposa adzalowa m’dziko la Kanani. Iwo aona zozizwitsa zimene ndinachita mu Igupto ndi m’chipululu, koma sakundikhulupirirabe. Chotero adzapupulika-pupulika m’chipululu kwa zaka 40 mpaka wotsirizira wa iwo atafa. Yoswa yekha ndi Kalebi adzalowa m’dziko la Kanani.