Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 39

Ndodo ya Aroni ichita Maluwa

Ndodo ya Aroni ichita Maluwa

ONANI maluwa’wo ndi katungulume wakupsya wobala pa ndodo’yi. Iyi ndi ndodo ya Aroni. Maluwa’wa ndi chipatso chakupsya’cho zinamera pa ndodo ya Aroni mu usiku umodzi wokha! Tiyeni tione chifukwa chake.

Aisrayeli akhala akupupulika-pupulika kwa kanthawi m’chipululu tsopano. Ena sakuganiza kuti Mose ayenera kukhala m’tsogoleri, kapena kuti Aroni ayenera kukhala mkulu wa ansembe. Kora ali mmodzi wa oganiza motere, chimodzi-modzi’nso Datani, Abiramu ndi atsogoleri a anthu okwanira 250. Onse’wa akudza nati kwa Mose: ‘Kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti inu mukudzikweza pa ife tonse?’

Mose akuuza Kora ndi atsatiri ake kuti: ‘Mawa m’mawa tengani mbale za moto ndi kuikamo lubani. Nimudze ku chihema chokomana’ko cha Yehova. Tidzaona amene Yehova akum’sankha.’

M’mawa mwake Kora ndi atsatiri ake 250 akudza ku chihema’ko. Ena’nso ambiri akudza kudzachirikiza amuna’wa. Yehova akupsya mtima kwambiri. ‘Tulukani m’mahema a anthu oipa’wa,’ anatero Mose. ‘Musakhudze kanthu kao kali konse.’ Anthu’wo anamvetsera, natalikirana ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.

Ndiyeno Mose akuti: ‘Mwa ichi mudzadziwa amene Yehova wasankha. Nthaka idzang’ambika ndi kumeza amuna oipa’wa.

Pamene Mose akungoleka kulankhula, nthaka ikuyasama. Hema wa Kora ndi zake zonse ndi Datani ndi Abiramu ndi onse okhala nawo akulowa pansi, nthaka niwaphimba. Anthu pakumva mfuu za awo ogwera pansi, akupfuula kuti: ‘Tiyeni tithawe! Lingamenze ife’nso dziko!’

Kora ndi atsatiri ake 250 akali pafupi ndi chihema chokomana’ko. Chotero Yehova akutumiza moto, onse’wo napsya. Ndiyeno Yehova akuuza mwana wa Aroni Eliezara kutenga mbale za moto za anthu akufa’wo ndi kupanga chobvundikirira guwa la nsembe chapanthi-phanthi. Chobvundikirira guwa la nsembe’chi chiyenera kukhala ngati chenjezo kwa Aisrayeli chakuti palibe wina kusiyapo Aroni ndi ana ake amuna amene ayenera kuchita monga ansembe a Yehova.

Koma Yehova akufuna kumveketsa bwino lomwe kuti Aroni ndi ana ake ndiwo amene iye wawasankha kukhala ansembe. Chotero akuuza Mose kuti: ‘Chititsa kalonga wa pfuko liri lonse kudza ndi ndodo yake. Kaamba ka pfuko la Levi, chita kuti Aroni adze ndi ndodo yake. Ndiyeno uike ndodo zonse’zi m’chihema chokumana’ko patsogolo pa likasa la chipangano. Ndodo ya munthu amene ndam’sankha idzachita maluwa.’

Poyang’ana Mose m’mawa mwake, onani, ndodo ya Aroni iri ndi maluwa ndi akatungulume akupsya otulukamo! Chotero kodi mukuona tsono chifukwa chake Yehova anachititsa ndodo ya Aroni kuchita maluwa?