Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 42

Bulu Alankhula

Bulu Alankhula

KODI munayamba mwamva kuti bulu analankhula? ‘Ai,’ mungatero. ‘Zinyama sizingalankhule.’ Koma Baibulo limasimba za bulu amene analankhula. Tiyeni tione m’mene zinachitikira.

Aisrayeli atsala pang’ono kulowa m’Kanani. Balaki, mfumu ya Moabu, ikuopa Aisrayeli. Chotero akutumiza munthu wochenjera wochedwa Balamu kukatemberera Aisrayeli. Balaki akulonjeza kupatsa Balamu ndalama zochuluka, chotero Balamu akukwera pa bulu wake namka ulendo wokaonana ndi Balaki.

Yehova sakufuna kuti Balamu atemberere anthu Ake. Chotero akutumiza mngelo wokhala ndi lupanga kukatsekereza Balamu. Balamu sakuona mngelo’yo koma bulu wake akuona. Chotero bulu’yo akuyesa kupewa mngelo’yo ndipo potsiriza akungogona pansi pa mseu. Balamu wapsya mtima kwambiri, ndipo akupanda bulu’yo ndi ndodo.

Kenako Yehova akuchititsa Balamu kumva bulu’yo akulankhula naye. ‘Ndakuchitanji kuti wandipanda katatu?’ akufunsa motero bulu’yo.

‘Wandiputsitsa,’ akutero Balamu. ‘N’kadakhala ndi lupanga n’kadakupha!’

‘Kodi n’dakuchitirapo zotere n’kale lonse?’ akufunsa tero bulu’yo.

Balamu akuyankha kuti, ‘Ai.’

Ndiyeno Yehova akuonetsa Balamu mngelo wokhala ndi lupanga woima pa njira’yo. Mngelo’yo akuti: ‘Wapandiranji bulu wako? Ndabwera kudzatsekereza njira yako, chifukwa suyenera kumka kukatemberera Israyeli. Bulu wako akadapanda kundipatukira, n’kadakukantha, koma sin’kadabvulaza bulu wako.’

Balamu akuti: ‘Ndachimwa. Sindinadziwe kuti mwaima panjira.’ Mngelo’yo akulola Balamu kupita, ndipo iye akupita kukaonana ndi Balaki. Iye akuyesabe kutemberera Israyeli, koma m’malo mwake, Yehova akum’chititsa kudalitsa Israyeli katatu.